Masalmo 61 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Poopsedwa Davide athamangira Mulungu

Kwa Mkulu wa Nyimbo; Neginoto. Salmo la Davide.

1. Imvani mpfuu wanga, Mulungu;Mverani pemphero langa.

2. Ku malekezero a dziko lapansi ndidzapfuulira kwa Inu, pomizika mtima wanga:Nditsogolereni ku thanthwe londiposa ine m'kutalika kwace.

3. Pakuti munakhala pothawirapo panga; nsanja yolimba pathawa mdani ine.

4. Ndidzagonera-gonerabe m'cihemamwanu;Ndidzathawira mobisalamo m'mapiko anu.

5. Pakuti Inu, Mulungu, mudamva zowinda zanga;Munandipatsa colowa ca iwo akuopa dzina lanu.

6. Mudzatalikitsa moyo wa mfumu:Zaka zace zidzafikira mibadwo mibadwo.

7. Adzakhala nthawi zonse pamaso pa Mulungu;Mumpatse cifundo ndi coonadi zimsunge.

8. Potero ndidzayimba zolemekeza dzina lanu ku nthawi zonse,Kuti ndicite zowinda zanga tsiku ndi tsiku.