Masalmo 134 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Afulumizidwa anthu kulemekeza Yehova

Nyimbo vokwerera,

1. Taonani, lemekezani Yehova, atumiki a Yehova inu nonse,Akuimirira m'nyumba ya Yehova usiku,

2. Kwezani manja anu ku malo oyera,Nimulemekeze Yehova.

3. Yehova, ali m'Ziyoni, akudalitseni;Ndiye amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi.