Masalmo 1 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Kusiyana pakati pa olungama ndi oipa

1. WODALA munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa,Kapena wosaimirira m'njira ya ocimwa,Kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza.

2. Komatu m'cilamulo ca Yehova muli cikondwerero cace;Ndipo m'cilamulo cace amalingima usana ndi usiku.

3. Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi;Wakupatsa cipatso cace pa nyengo yace,Tsamba lace lomwe losafota;Ndipo zonse azicita apindula nazo.

4. Oipa satero ai;Koma akunga mungu wouluka ndi mphepo.

5. Cifukwa cace oipa sadzaimirira pa mlanduwo,Kapena ocimwa mu msonkhano wa olungama.

6. Pakuti Yehova adziwa mayendedwe a olungama;Koma mayendedwe a oipa adzatayika.