Masalmo 43 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Davide alira akhale ku Kacisi

1. Mundiweruzire, Mulungu, ndipo mundinenere mlandu kwa anthu opanda cifundo:Mundilanditse kwa munthu wonyenga ndi wosalungama.

2. Pakuti Inu ndinu Mulungu wa mphamvu yanga; mwanditayiranji?Ndimayenderanji woliralira cifukwa ca kundipsinja mdani?

3. Tumizirani kuunika kwanu ndi coonadi canu zinditsogolere:Zindifikitse ku phiri lanu loyera,Kumene mukhala Inuko.

4. Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu,Kufikira Mulungu wa cimwemwe canga ceniceni:Ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga.

5. Udziweramiranji moyo wanga iwe?Ndi kuzingwa m'kati mwanga?Yembekeza Mulungu: pakuti ndidzamyamikanso,Ndiye cipulumutso ca nkhope yanga, ndi Mulungu wanga.