Masalmo 126 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Ayamikira mokondwerera kuti Mulungu anabweza ukapolo wao

Nyimbo yokwerera.

1. Pobweza Yehova ukapolo wa Ziyoni,Tinakhala ngati anthu akulota.

2. Pamenepo pakamwa pathu panadzala ndi kuseka,Ndi lilime lathu linapfuula mokondwera;Pamenepo anati mwa amitundu,Yehova anawacitira iwo zazikuru,

3. Yehova anaticitira ife zazikuru;Potero tikhala okondwera.

4. Bwezani ukapolo wathu, Yehova,Ngati mitsinje ya ku Mwera.

5. Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kupfuula mokondwera.

6. Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbeu yakufesa;Adzabweranso ndithu ndi kupfuula mokondwera, alikunyamula mitolo yace.