11. Pamenepo Yefita anamuka ndi akuru a Gileadi, ndipo anthu anamuika mkuru wao ndi mtsogoleri wao; ndipo Yefita ananena mau ace onse pamaso pa Yehova ku Mizipa.
12. Ndipo Yefita anatuma mithenga kwa mfumu ya ana a Amoni, ndi kuti, Ndi ciani ndi Inu, ndi kuti Mwandidzera kuthira nkhondo dziko langa?
13. Ndipo mfumu ya ana a Amoni inati kwa mithenga ya Yefita, Cifukwa Israyeli analanda dziko langa pakukwera iye kucokera ku Aigupto, kuyambira Arinoni mpaka Yaboki, ndi mpaka Yordano; ndipo tsopano uodibwezere maikowa mwamtendere.
14. Ndipo Yefita anatumanso mithenga kwa mfumu ya ana a Amoni;
15. nanena naye, Atero Yefita, Israyeli sanalanda dziko la Moabu kapena dziko la ana a Amoni;
16. pakuti pakukwera iwo kucokera ku Aigupto Israyeli anayenda m'cipululu mpaka Nyanja Yofiira, nafika ku Kadesi;
17. pamenepo Israyeli anatuma mithenga kwa mfumu ya Edomu, ndi kuti, Ndikupemphani ndipitire pakati pa dziko lanu; koma mfumu ya Edomu sinamvera. Natumanso kwa mfumu ya Moabu; nayenso osalola; ndipo Israyeli anakhala m'Kadesi.
18. Pamenepo anayenda m'cipululu, naphazira dziko la Edomu, ndi dziko la Moabu, nadzera kum'mawa kwa dziko la Moabu, namanga misasa tsidya lija la Arinoni; osalowa malire a Moabu, pakuti Arinoni ndi malire a Moabu.
19. Ndipo Israyeli anatuma mithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, mfumu ya ku Hesiboni; nanena naye Israyeli, Tikupemphani tipitire pakati pa dziko lanu, kumka kwathu.
20. Koma Sihoni sanakhulupirira Israyeli kuti apitire pakati pa malire ace; koma Sihoni anamemeza anthu ace onse, namanga misasa ku Yahazi, nathira nkhondo Israyeli.
21. Ndipo Yehova Mulungu wa Israyeli anapereka Sihoni ndi anthu ace onse m'dzanja la Israyeli, ndipo anawakantha, ndi Israyeli analandira colowa cace, dziko lonse la Aamori, nzika za m'dziko lija.
22. Ndipo analandira akhale colowa cao, malire onse a Aamori, kuyambira Arihoni mpaka Yaboki, ndi kuyambira cipululu mpaka Yordano.
23. Motero Yehova Mulungu wa Israyeli anaingitsa Aamori, pamaso pa anthu ace Israyeli, ndipo kodi liyenera kukhala colowa canu?
24. Cimene akulandiritsani Kemosi mulungu wanu, simucilandira colowa canu kodi? Momwemo ali yense Yehova Mulungu wathu waiogitsa pamaso pathu, zacezo tilandira colowa cathu.
25. Ndipo tsopano kodi inu ndinu wabwino woposa Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Moabu; anatengana konse ndi Israyeli iyeyu kodi, kapena kucita nao nkhondo konse kodi?
26. Pokhala Israyeli m'Hesiboni ndi midzi yace, ndi m'Aroeri ndi midzi yace, ndi m'midzi yonse yokhala m'mphepete mwa Arinoni zaka mazana atatu; munalekeranji kulandanso nthawi ija?
27. Potero sindinakucimwirani ine, koma mundicitira coipa ndinu kundithira nkhondo; Yehova, Woweruzayo, aweruze lero lino pakati pa ana a Israyeli ndi ana a Amoni.
28. Koma mfumu ya ana a Amoni sanamvera mau a Yefita anamtumizirawo.
29. Pamenepo mzimu wa Yehova unamdzera Yefita, napitira iye ku Gileadi, ndi Manase, napitira ku Mizipa wa Gileadi, ndi kucokera ku Mizipa wa Gileadi anapitira kwa ana a Amoni.
30. Ndipo Yefita anawindira Yehova cowinda, nati, Mukaperekatu ana a Amoni m'dzanja langa, ndipo kudzali kuti ciri conse cakuturuka pakhomo pa nyumba yanga kudzakomana nane pakubweranso ine ndi mtendere kucokera kwa ana a Amoni, cidzakhala ca Yehova, ndipo ndidzacipereka nsembe yopsereza.