Pamenepo anayenda m'cipululu, naphazira dziko la Edomu, ndi dziko la Moabu, nadzera kum'mawa kwa dziko la Moabu, namanga misasa tsidya lija la Arinoni; osalowa malire a Moabu, pakuti Arinoni ndi malire a Moabu.