pamenepo Israyeli anatuma mithenga kwa mfumu ya Edomu, ndi kuti, Ndikupemphani ndipitire pakati pa dziko lanu; koma mfumu ya Edomu sinamvera. Natumanso kwa mfumu ya Moabu; nayenso osalola; ndipo Israyeli anakhala m'Kadesi.