Oweruza 8:11-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo Gideoni anakwerera njira ya iwo okhala m'mahema kum'mawa kwa Noba, ndi Yogibea, nakantha khamulo popeza khamulo linakhala lokhazikika mtima.

12. Ndipo Zeba ndi Tsalimuna anathawa; koma anawatsata, nagwira mafumu awiri a Midyani Zeba ndi Tsalimuna, nanjenjemeretsa khamu lonse.

13. Pamenepo Gideoni mwana wa Yoasi anabwerera kunkhondo pokwerera pa Heresi.

14. Ndipo anagwira mnyamata wa anthu a ku Sukoti, nafunsira; ndipo anamsimbira akalonga a ku Sukoti, ndi akulu ace amuna makumi asanu ndi awiri kudza asanu ndi awiri.

15. Ndipo anafika kwa amuna a ku Sukoti, nati, Tapenyani Zeba ndi Tsalimuna amene munanditonza nao ndi kuti, Kodi manja a Zeba ndi Tsalimuna akhala m'dzanja lako, kuti tiwaninkhe mkate amuna ako akulema?

16. Ndipo anagwira akulu, a m'mudzi ndi minga ya kucipululu ndi mitungwi, nawalanga nazo amuna a ku Sukoti.

17. Ndipo anagamula nsanja ya Penueli, napha amuna a kumudzi.

18. Pamenepo anati kwa Zeba ndi Tsalimuna, Amunawo munawapha ku Tabori anali otani? Iwo nayankha, Monga iwe momwemo iwowa; yense wakunga mwana wa mfumu.

19. Ndipo anati, Ndiwo abale anga, ana a mai wanga. Pali Yehova mukadawasunga amoyo, sindikadakuphani.

20. Nati kwa Yeteri mwana wace woyamba, Tauka, nuwaphe. Koma mnyamatayo sanasolola lupanga lace; pakuti anaopa, pokhala anali mnyamata.

21. Pamenepo Zeba ndi Tsalimuna anati, Tauka iwe mwini nutigwere; pakuti monga munthu momwemo mphamvu yace. Ndipo Gideoni anauka nawapha Zeba ndi Tsalimuna, nalanda mphande zinali kukhosi kwa ngamila zao.

22. Pamenepo anthu a Israyeli anati kwa Gideoni, Mutilamulire ndi inu, ndi mwana wanu, ndi mdzukulu wanu, pakuti mwatipulumutsa m'dzanja la Amidyani.

23. Koma Gideoni ananena nao. Sindidzalamulira inu, ngakhale mwana wanga sadzalamulira inu; Yehova adzalamulira inu.

24. Gideoni anatinso kwa iwo, Mundilole ndipemphe kanthu kamodzi kwa inu, mundipatse ali yense mapelele mwa zofunkha zanu; pakuti anali nao mapelele agolidi, pokhala anali Aismayeli.

25. Ndipo anayankha, Kupereka tiwapereka; nayalapo cobvala, naponyamo yense mapelele a mwa zofunkha zao.

26. Ndipo kulemera kwace kwa mapelele agolidi adawapempha ndiko masekeli cikwi cimodzi ndi mazana asanu ndi awiri; osawerenga mphande, ndi zitunga ndi zobvala zacibakuwa za pa mafumu a ku Midyani, osawerenganso maunyolo okhala pa makosi a ngamila zao.

27. Ndipo Gideoni anawapanga fano, naliika m'mudzi mwace, ndiwo Ofira; ndi Israyeli yense analitsata kuligwadira pomwepo; ndipo linakhala kwa Gideoni ndi nyumba yace ngati msampha.

28. Motero anagonjetsa Amidyani pamaso pa ana a Israyeli, osaweramutsanso mitu yao iwowa. Ndipo dziko lidapumula zaka makumi anai m'masiku a Gideoni.

29. Ndipo Yerubaala, mwana wa Yoasi anamuka, nakhala, m'nyumba ya iye yekha.

Oweruza 8