1. Koma amuna a Israyeli adalumbira ku Mizipa, ndi kuti, Palibe mmodzi wa ife adzapereka mwana wace wamkazi kwa Mbenjamini akhale mkazi wace.
2. Ndipo anthu anadza ku Beteli, nakhala pansi pomwepo pamaso pa Mulungu mpaka madzulo; nakweza mau ao ndi kulira misozi yambiri.
3. Nati iwo, Yehova Mulungu wa Israyeli, cacitika ici cifukwa ninji m'Israyeli kuti lasowa lero pfuko limodzi m'Israyeli?
4. Ndipo kunali m'mawa mwace, anthu analawirira mamawa namangako guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika.
5. Nati ana a Israyeli, Ndani iye mwa mapfuko onse a Israyeli amene sanakwera kudza kumsonkhano kwa Yehova? pakuti panali lumbiro lalikuru pa iye wosakwera kudza kwa Yehova ku Mizipa, ndi kuti, Aphedwe ndithu.
6. Ndipo ana a Israyeli anamva cifundo cifukwa ca Benjamini mbale wao, nati, Pfuko limodzi lalikhidwa pa Israyeli leroli.
7. Tidzatani kuwafunira otsalawo akazi, popeza tinalumbira ife pa Yehova kuti sitidzawapatsa ana athu akazi akhale akazi ao?
8. Nati iwo, Kodi pali lina la mapfuko a Israyeli losakwera kudza kwa Yehova ku Mizipa? Ndipo taonani, kucokera ku Yabesi-gileadi sanadza mmodzi kumisasa, kumsonkhano.
9. Pakuti pamene anawerenga anthu, taonani, panalibe mmodzi komweko wa okhala m'Yabesi-gileadi,
10. Ndipo msonkhano unatumizako amuna zikwi khumi ndi ziwiri, ndiwo ngwazi, nawalamulira ndi kuti, Mukani, nimuwakanthe okhala m'Yabesi-gileadi ndi lupanga lakuthwa, ndi akazi ndi ana ang'ono.
11. Ndipo cimene mukacite ndi ici: mukaononge konse mwamuna ali yense, ndi mkazi ali yense wodziwa mwamuna mogona naye.
12. Ndipo anapeza mwa anthu a Yabesi-gileadi anamwali mazana anai osadziwa mwamuna mogona naye; nabwera nao kumisasa ku Silo, ndiwo a m'dziko la Kanani.
13. Ndipo msonkhano wonse unatumiza mau kwa ana a Benjamini okhala m'thanthwe la Rimoni, nawalalikira mtendere.