Nati ana a Israyeli, Ndani iye mwa mapfuko onse a Israyeli amene sanakwera kudza kumsonkhano kwa Yehova? pakuti panali lumbiro lalikuru pa iye wosakwera kudza kwa Yehova ku Mizipa, ndi kuti, Aphedwe ndithu.