1. Ndipo kunali, masiku aja, pamene panalibe mfumu m'Israyeli, panali munthu Mlevi wogonera kutseri kwa mapiri a Efraimu amene anadzitengera mkazi wamng'ono wa ku Betelehemu-Yuda.
2. Koma mkazi wace wamng'ono anacita cigololo akali naye, namcokera kumka ku nyumba ya atate wace ku Betelehemu-Yuda, nakhalako nthawi ya miyezi inai.
3. Koma anauka mwamuna wace namtsata kukamba naye zamtima, kumbwezanso; napita ndi mnyamata wace, ndi aburu awiri. Ndipo mkaziyo anadza naye ku nyumba ya atate wace. Ndipo pakumuona atate wa mkaziyo, anakondwera kukomana naye.
4. Ndipo mpongozi wace, ndiye atate wa mkaziyo, anamuimika kuti akhale naye masiku atatu; nadya namwa nagona komweko.
5. Ndipo kunali, tsiku lacinai, analawirira mamawa, nanyamuka iye kucoka; koma atate wa mkaziyo anati kwa mkamwini wace, Limbitsa mtima wako ndi mkate pang'ono, ndipo utatero upite.
6. Nakhala pansi nadya namwa onse awiri pamodzi; nati kwa munthuyo atate wa mkaziyo, Ubvomere, ugone kuno usiku, nusekerere mtima wako.
7. Ndipo munthuyo ananyamuka kuti amuke; koma mpongozi waceyo anamkakamiza, nagonanso komweko.
8. Nalawirira mamawa tsiku lacisanu kuti amuke, koma atate wa mkaziyo anati, Ulimbitse mtima wako, nulindire lipendeke dzuwa; nadya iwo onse awiri.
9. Pamenepo munthuyo ananyamuka kucoka, iye ndi mkazi wace wamng'ono ndi mnyamata wace; koma mpongozi wace, atate wa mkaziyo, ananena naye, Tapenya, lapendeka dzuwa, ugone kuno usiku; tapenya lapendekatu dzuwa, ugone kuno, nusekerere mtima wako; nimulawire mamawa kumka ulendo wanu kwanu.
10. Koma munthuyo anakana kugonako usiku, nanyamuka, nacoka, nadza pandunji pa Yebusi (ndiwo Yerusalemu); ndi pamodzi naye panali aburu awiri omangirira mbereko; anali nayenso mkazi wace wamng'ono.
11. Pofika iwo pa Yebusi linalimkulowa dzuwa, ndi mnyamata anati kwa mbuye wace, Tiyeni, tipambukire mudzi uwu wa Ayebusi ndi kugona pomwepa.