Pamenepo anaturuka ana onse a Israyeli, nuunjikana msonkhano kwa Yehova ku Mizipa ngati munthu mmodzi, kuyambira ku Dani mpaka Beereseba ndi dziko la Gileadi lomwe.