Mateyu 4:5-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Pamenepo mdierekezi anamuka naye ku mzinda woyera; namuika Iye pamwamba pa cimbudzi ca Kacisi,

6. nanena naye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, mudzigwetse nokha pansi: pakuti kwalembedwa, kuti,Adzauza angelo ace za iwe,Ndipo pa manja ao adzakunyamulaiwe,Ungagunde konse phazi lako pamwala.

7. Yesu ananena naye, Ndiponso kwalembedwa,Usamuyese Ambuye Mulungu wako.

8. Pomwenso mdierekezi anamuka naye ku phiri lalitari, namuonetsa maiko onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wao;

9. nati kwa Iye, Zonse ndikupatsani Inu, ngati mudzagwa pansi ndi kundigwadira ine.

10. Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Coka Satana, pakuti kwalembedwa,Ambuye Mulungu wako udzamgwadira,Ndipo Iye yekha yekha udzamlambira.

11. Pomwepo mdierekezi anamsiya Iye, ndipo onani, angelo anadza, namtumikira Iye.

12. Ndipo pamene Yesu anamva kuti anampereka Yohane, anamuka kulowa ku Galileya;

13. ndipo anacoka ku Nazarete nadza nakhalitsa Iye m'Kapernao ira pambali pa nyanja, m'malire a Zebuloni ndi Nafitali:

14. kuti cikacitidwe conenedwa ndi Yesaya mneneri, kuti,

15. It Dziko la Zebuloni ndi dziko la N afitali,Njira ya kunyanja, kutsidya lija la Yordano,Galileya la anthu akunja,

16. Anthu akukhala mumdimaAdaona kuwala kwakukuru,Ndi kwa iwo okhala m'malo mthunzi wa imfa,Kuwala kunaturukira iwo.

17. Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kulalikira, ndi kunena, Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wa Kumwamba wayandikira.

18. Ndipo pamene Yesu analikuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wonenedwa Petro, ndi Andreya, mbale wace, analikuponya psasa m'nyanja; popeza anali asodzi a nsomba.

19. Ndipo Iye ananena nao, Tiyeni pambuyo panga, ndidzakusandutsani asodzi a anthu.

20. Ndipo iwo anasiya pomwepo makokawo, namtsata Iye.

21. Ndipo popitirirapo Iye anaona abale ena awiri, Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi Yohane mbale wace, m'ngalawa, pamodzi ndi Zebedayo atate wao, analikusoka makoka ao; ndipo anaitana iwo.

Mateyu 4