Mateyu 4:12-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo pamene Yesu anamva kuti anampereka Yohane, anamuka kulowa ku Galileya;

13. ndipo anacoka ku Nazarete nadza nakhalitsa Iye m'Kapernao ira pambali pa nyanja, m'malire a Zebuloni ndi Nafitali:

14. kuti cikacitidwe conenedwa ndi Yesaya mneneri, kuti,

15. It Dziko la Zebuloni ndi dziko la N afitali,Njira ya kunyanja, kutsidya lija la Yordano,Galileya la anthu akunja,

16. Anthu akukhala mumdimaAdaona kuwala kwakukuru,Ndi kwa iwo okhala m'malo mthunzi wa imfa,Kuwala kunaturukira iwo.

17. Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kulalikira, ndi kunena, Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wa Kumwamba wayandikira.

18. Ndipo pamene Yesu analikuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wonenedwa Petro, ndi Andreya, mbale wace, analikuponya psasa m'nyanja; popeza anali asodzi a nsomba.

19. Ndipo Iye ananena nao, Tiyeni pambuyo panga, ndidzakusandutsani asodzi a anthu.

20. Ndipo iwo anasiya pomwepo makokawo, namtsata Iye.

21. Ndipo popitirirapo Iye anaona abale ena awiri, Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi Yohane mbale wace, m'ngalawa, pamodzi ndi Zebedayo atate wao, analikusoka makoka ao; ndipo anaitana iwo.

22. Ndipo anasiya pomwepo ngalawayo ndi atate wao, namtsata Iye.

23. Ndipo Yesu anayendayenda m'Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira uthenga wabwino wa Ufumu, naciritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.

Mateyu 4