31. Ndipo ankhondo adzamuimirira, nadzadetsa malo opatulika ndi linga lace; nadzacotsa nsembe yosalekezayo, nadzaimitsa conyansa copululutsaco.
32. Ndipo akucitira coipa cipanganoco iye adzawaipsa, ndi kuwasyasyalika; koma anthu akudziwa Mulungu wao adzalimbika mtima, nadzacita mwamphamvu.
33. Ndipo aphunzitsi a anthu adzalangiza ambiri, koma adzagwa ndi lupanga, ndi lawi lamoto, ndi undende, ndi kufunkhidwa masiku ambiri.
34. Ndipo pakugwa iwo adzathandizidwa ndi thandizo laling'ono; koma ambiri adzaphatikizana nao ndi mau osyasyalika.
35. Nadzagwa aphunzitsi ena kuwayesa ndi moto, ndi kuwatsutsa, ndi kuwayeretsa, mpaka nthawi ya citsiriziro; pakuti kukaliko kufikira nthawi yoikika.
36. Ndipo mfumu idzacita monga mwa cifuniro cace, nidzadzikweza, ndi kudzikuza koposa milungu iri yonse nidzanena zodabwiza pa Mulungu wa milungu, nidzapindula, mpaka udzacitidwa ukaliwo; pakuti cotsimikizika m'mtimaco cidzacitika.
37. Ndipo sidzasamalira milungu ya makolo ace, kapena coikhumba akazi, kapena kusamalira milungu iri yonse; pakuti idzadzikuza koposa onse.
38. Koma kumalo kwace idzacitira ulemu mulungu wa malinga; ndi mulungu amene makolo ace sanaudziwa, adzaulemekeza ndi golidi, ndi siliva, ndi miyala ya mtengo wace, ndi zinthu zofunika.
39. Ndipo adzacita molimbana ndi malinga olimba koposa, pomthandiza mulungu wacilendo; ali yense wombvomereza adzamcurukitsira ulemu, nadzawacititsa ufumu pa ambiri, nadzagawa dziko mwa mtengo wace.