2 Samueli 10:5-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Pamene anaciuza Davide iye anatumiza anthu kukakomana nao; pakuti amunawo anacita manyazi akuru. Niti mfumu, Bakhalani ku Yeriko kufikira zamera ndebvuzanu; zitameramubwere.

6. Ndipo pamene ana a Amoni anazindikira kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, ana a Amoniwo anatumiza nadzilembera Aaramu a ku Betirehobu, ndi Aaramu a ku Zoba, oyenda pansi zikwi makumi awiri, ndi mfumu ya ku Maaka ndi anthu cikwi cimodzi, ndi anthu a mfumu ya ku Tobu zikwi khumi ndi ziwiri.

7. Ndipo pamene Davide anacimva, anatumiza Yoabu ndi khamu lonse la anthu amphamvu.

8. Ndipo ana a Amoni anaturuka, nandandalitsa nkhondo polowera kucipata. Ndipo Aaramu a ku Zoba ndi a ku Rehobu, ndi anthu a Tobu ndi Maaka, anali pa okha kuthengo.

9. Ndipo pamene Yoabu anaona kuti nkhondo inamdzera kumaso ndi kumbuyo, iye anasankha amuna osankhidwa onse a Israyeli, nawandandalitsa ca kwa Aramu.

10. Koma anthu otsalawo anawapereka kwa Abisai mbale wace, amene anawandandalitsa ca kwa Amoni.

11. Ndipo iye anati, Aaramu akandipambana ine, udzandithandiza ndiwe, koma ana a Amoni akapambana iwe, tsono ndidzabwera ine kukuthandiza.

12. Ulimbike mtima, ndipo ticite camuna lero cifukwa ca anthu athu ndi midzi ya Mulungu wathu; Yehova nacite comkomera.

13. Comweco Yoabu ndi anthu amene anali naye anayandikira kuponyana nkhondo ndi Aaramu. Ndipo iwowa anathawa pamaso pace.

14. Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti Aaramu anathawa, iwonso anathawa pamaso pa Abisai, nalowa m'mudzimo. Ndipo Yoabu anabwera kucokera kwa ana a Amoni, nafika ku Yerusalemu.

15. Ndipo pamene Aaramu anaona kuti Aisrayeli anawathyola, anasonkhana pamodzi.

16. Ndipo Hadarezeri anatumiza mthenga nakatenga Aaramu a ku tsidya la cimtsinje; iwo nafika ku Helamu, ndi Sobaki kazembe wa khamu la nkhondo la Hadarezeri anawatsogolera.

17. Ndipo wina anauza Davide; iye nasonkhanitsa Aisrayeli onse, naoloka Yordano nafika ku Helemu, Ndipo Aaramu anandandalitsa nkhondo yao pa Davide namenyana naye.

18. Ndipo Aaramu anathawa pamaso pa Israyeli; Davide naphapo Aaramu apamagareta mazana asanu ndi awiri, ndi apakavalo zikwi makumi anai, nakantha Sobaki kazembe wa khamu lao, nafa iye pomwepo.

2 Samueli 10