5. Ndipo iye anali munthu wakufuna Mulungu masiku a Zekariya, ndiye wozindikira masomphenya a Mulungu; ndipo masiku akufunira Yehova iye, Mulungu anamlemereza;
6. popeza anaturuka, nayambana ndi Afilisti, nagamula linga la Gati, ndi linga la Yabine, ndi linga la Asidodi; namanga midzi m'dziko la Asidodi, ndi mwa Afilisti.
7. Ndipo Mulungu anamthandiza poyambana ndi Afilisti, ndi Aarabu okhala m'Guribaala, ndi Ameuni.
8. Ndipo Aamoni anampatsa Uziya mitulo; ndi dzina lace linabuka mpaka polowera ku Aigupto; pakuti analil mbika cilimbikire.
9. Uziya anamanganso nsanja m'Yerusalemu pa cipata ca kungondya, ndi pa cipata ca kucigwa, ndi popindika linga; nazilimbikitsa.
10. Namanga nsanja m'cipululu, nakumba zitsime zambiri; popeza anali nazo zoweta zambiri; kumadambo, ndi kuzidikha; nakhala nao olima minda, ndi osunga mpesa kumapiri ndi ku nthaka yopatsa bwino; pakuti ndiye mlimi.
11. Uziya anali nalonso khamu la anthu a nkhondo, oturuka kunkhondo magulu; nawawerenga monga mwa mawerengedwe ao ndi dzanja la mlembi Yeyeli, ndi kapitao Maseya, monga anawauza Hananiya kazembe wina wa mfumu.
12. Ciwerengo conse ca akuru a nyumba za makolo, ndiwo ngwazi zamphamvu, ndico zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi.
13. Ndipo m'dzanja mwao munali khamu la nkhondo zikwi mazana atatu mphambu zikwi zisanu ndi ziwiri kudza mazana asanu ocita nkhondo ndi mphamvu yaikuru, kuthandiza mfumu alimbane ndi adani.
14. Ndipo Uziya anawakonzeratu ankhondo onse zikopa, ndi mikondo, ndi zisoti zacitsulo, ndi maraya acitsulo, ndi mauta, ndi miyala yoponyera.
15. Napanga m'Yerusalemu makina, opangidwa ndi eni luso, akhale pansanja ndi kungondya, aponye nao mibvi ndi miyala yaikuru. Ndi dzina lace linamveka kutali; pakuti anathandizidwa modabwiza, mpaka analimbikatu.
16. Koma atakhala wamphamvu, mtima wace unakwezeka momuononga, nalakwira Yehova Mulungu wace; popeza analowa m'Kacisi wa Yehova kufukiza pa guwa la nsembe la cofukiza.
17. Ndipo Azariya wansembe analowa pambuyo pace, ndi pamodzi naye ansembe a Yehova makumi asanu ndi atatu, ndiwo olimba mtima;
18. natsutsana ndi mfumu Uziya, nati kwa iye, Sikuyenera inu, Uziya, kufukizira Yehova, koma ansembe, ana a Aroni opatulidwira kufukiza; turukani m'malo opatulika; pakuti mwalakwa; Yehova Mulungu sakulemekezanipo.