5. Iwo afungatira mazira a mamba aswetse, naluka ukonde wa tandaude; iye amene adya mazira ace amafa, ndi coswanyikaco cisweka nicikhala songo.
6. Maukonde ao sadzakhala zobvala, sadzapfunda nchito zao; nchito zao ziri nchito zoipa, ndi ciwawa ciri m'manja mwao.
7. Mapazi ao athamangira koipa, ndipo iwo afulumira kukhetsa mwazi wosacimwa; maganizo ao ali maganizo oipa; bwinja ndi cipasuko ziri m'njira mwao.
8. Njira ya mtendere saidziwa, ndipo palibe ciweruziro m'mayendedwe mwao; akhotetsa njira zao; ali yense ayenda m'menemo sadziwa mtendere.
9. Cifukwa cace ciweruziro ciri patari ndi ife, ndi cilungamo sicitipeza; tiyang'anira kuunika, koma taona mdima; tiyang'anira kuyera, koma tiyenda m'usiku.
10. Tiyambasira khoma ngati wakhungu, inde tiyambasa monga iwo opanda maso; tipunthwa usana monga m'cizirezire; tiri m'malo amdima ngati akufa.
11. Tonse tibangula ngati zirombo, ndi kulira maliro zolimba ngati nkhunda; tiyang'anira ciweruziro koma palibe; tiyang'anira cipulumutso koma ciri patari ndi ife.
12. Pakuti zolakwa zathu zacuruka pamaso pa Inu, ndipo macimo athu atineneza ife; pakuti zolakwa zathu ziri ndi ife, ndipo zoipa zathu tizidziwa;
13. ndizo kulakwabe ndi kukanabe Yehova, ndi kuleka kutsata Mulungu wathu, kulankhula zotsendereza ndi kupanduka, kuganizira ndi kunena pakamwa mau akunyenga oturuka mumtima.