7. Ndipo Yehova anati kwa Gideoni, Ndi anthu mazana atatu akukhatira ndidzakupulumutsani, ndi kupereka Amidyani m'dzanja lako; koma amuke anthu awa onse, yense kumalo kwace.
8. Pamenepo anthu anatenga kamba m'dzanja lao, ndi malipenga ao; ndipo anauza amuna onse a Israyeli amuke, yense kuhema kwace; koma anaimika amuna mazana atatuwo; ndipo misasa ya Midyani inali kunsi kwace m'cigwa.
9. Ndipo kunali usiku womwewo, kuti Yehova ananena naye, Tauka, tatsikira kumisasa; pakuti ndaipereka m'dzanja lako.
10. Koma ngati uopa kutsika, utsike naye Pura mnyamata wako kumisasa;
11. nudzamva zonena iwo; utatero manja ako adzalimbikitsidwa kutsikira kumisasa. Pamenepo anatsikira ndi Pura mnyamata wace ku cilekezero ca anthu azidaa m'misasa.
12. Ndipo Amidyani ndi Aamaleki ndi ana onse a kum'mawa ali gonere m'cigwa, kucuruka kwao ngati dzombe; ndi ngamila zao zosawerengeka, kucuruka kwao ngati mcenga wa m'mphepete mwa nyanja.
13. Ndipo pakufikako Gideoni, taonani, panali munthu analikufotokozera mnzace loto, nati, Taona, kulota ndinalota, ndipo tapenya, mtanda wa mkate wabarele unakunkhulira-kunkhulira m'misasa ya Midyani, nufika kuhema, numgunda nagwa, numpidigula kuti hema anakhala cigwere.
14. Ndipo mnzace anayankha nati, Ici si cina konse koma lupanga la Gideoni mwana wa Yoasi, munthu wa Israyeli; Mulungu wapereka Midyani ndi a m'misasa onse m'dzanja lace.
15. Ndipo kunali, pakumva Gideoni kufotokozera kwa lotolo ndi tanthauzo lace, anadziwerama; nabwera ku misasa ya Israyeli nati, Taukani, pakuti Yehova wapereka a m'misasa a Midyani m'dzanja lanu.
16. Ndipo anagawa amuna mazana atatu akhale magulu atatu, napatsa malipenga m'manja a iwo onse, ndi mbiya zopanda kanthu, ndi miuni m'kati mwa mbiyazo,
17. Ndipo ananena nao, Mundipenyerere ine, ndi kucita momwemo; ndipo taonani, pakufika ine pa cilekezero ca misasa, kudzali, monga ndicita ine, momwemo muzicita inu.
18. Pamene ndiomba lipenga, ine ndi onse okhala nane, inunso muziomba lipenga pozungulira ponse pa misasa, ndi kunena kuti, Yehova ndi Gideoni.
19. Motero Gideoni ndi amuna zana anali naye anafikira ku cilekezero ca misasa poyambira ulonda wa pakati, atasintha alonda tsopano apa; ndipo anaomba malipenga, naphwanya mbiya zokhala m'manja mwao.
20. Ndi magulu atatuwo anaomba malipenga, naswa mbiyazo, nagwira miuni ndi dzanja lao lamanzere, ndi malipenga m'dzanja lao lamanja kuwaomba; ndipo anapfuula, Lupanga la Yehova ndi la Gideoni.
21. Ndipo anaima yense m'mbuto mwace pozungulira misasa; pamenepo anathamanga a m'misasa onse, napfuula, nathawa.