23. Ndipo Yehova anati kwa iye, Mtendere ukhale ndi iwe, usaope, sudzafa.
24. Pamenepo Gideoni anammangira Yehova guwa la nsembe pomwepo; nalicha Yehova-ndiyemtendere; likali m'Ofira wa Abieziri ndi pano pomwe.
25. Ndipo kunali, usiku womwe uja Yehova ananena naye, Tenga ng'ombe ya atate wako, ndiyo ng'ombe yaciwiri ya zaka zisanu ndi ziwiri, nugamule guwa la nsembe la Baala ndilo la atate wako, nulikhe cifanizo ciri pomwepo;
26. numangire Yehova Mulungu wako guwa la nsembe pamwamba pa lingali, monga kuyenera; nutenge ng'ombe yaciwiriyo, nufukize nsembe yopsereza; nkhuni zace uyese cifanizo walikhaco.
27. Pamenepo Gideoni anatenga amuna khumi mwa anyamata ace, nacita monga Yehova adanena naye; ndipo kunali, popeza anaopa a ku nyumba ya atate wace, ndi amuna a ku mudziwo, sanacicita msana, koma usiku.
28. Ndipo pakuuka mamawa amuna a ku mudziwo, taonani, guwa la nsembe la Baala litagamuka, ndi cifanizo cinali pomwepo citalikhidwa ndi ng'ombe yaciwiri yoperekedwa pa guwa la nsembe adalimanga.
29. Nanenana wina ndi mnzace, Wacita ici ndani? Ndipo atafunafuna nafunsafunsa, anati, Gideoni, mwana wa Yoasi wacita ici.
30. Pamenepo amuna a ku mudziwo anati kwa Yoasi, Umturutse mwana wako kuti afe; pakuti anagamula guwa la nsembe la Baala, pakutinso analikha cifanizo cinali pomwepo.
31. Koma Yoasi anati kwa onse akumuimirira, Kodi inu mumnenera Baala mlandu? Kapena kodi mudzampulumutsa iye? iye amene amnenera mlandu aphedwe kukali m'mawa; akakhala mulungu adzinenere yekha mlandu, popeza wina wamgamulira guwa lace la nsembe.
32. Cifukwa cace anamucha tsiku lija Yerubaala, ndi kuti, Amnenece mlandu Baala popeza anamgamulira guwa lace la nsembe.
33. Pamenepo Amidyani onse ndi Aamaleki ndi ana a kum'mawa anasonkhana pamodzi naoloka, namanga misasa m'cigwa ca Yezreeli.
34. Koma mzimu wa Yehova unabvana Gideoni; naomba lipenga iye, ndi a banja la Abieziri analalikidwa kumtsata iye.
35. Ndipo anatuma mithenga kwa Manase konse; ndi iwonso analalikidwa kumtsata iye; natuma mithenga kwa Aseri, ndi kwa Zebuloni, ndi kwa Nafitali; iwo nadzakomana nao.
36. Ndipo Gideoni anati kwa Mulungu, Mukadzapulumutsa Israyeli ndi dzanjalanga monga mwanena,