Pamenepo Yerubaala, ndiye Gideoni, ndi anthu onse okhala naye anauka mamawa, namanga misasa pa citsime ca Harodi, ndi misasa ya Midyani inali kumpoto kwao, pa phiri la More m'cigwa.