Pamenepo Gideoni anatenga amuna khumi mwa anyamata ace, nacita monga Yehova adanena naye; ndipo kunali, popeza anaopa a ku nyumba ya atate wace, ndi amuna a ku mudziwo, sanacicita msana, koma usiku.