Oweruza 19:4-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo mpongozi wace, ndiye atate wa mkaziyo, anamuimika kuti akhale naye masiku atatu; nadya namwa nagona komweko.

5. Ndipo kunali, tsiku lacinai, analawirira mamawa, nanyamuka iye kucoka; koma atate wa mkaziyo anati kwa mkamwini wace, Limbitsa mtima wako ndi mkate pang'ono, ndipo utatero upite.

6. Nakhala pansi nadya namwa onse awiri pamodzi; nati kwa munthuyo atate wa mkaziyo, Ubvomere, ugone kuno usiku, nusekerere mtima wako.

7. Ndipo munthuyo ananyamuka kuti amuke; koma mpongozi waceyo anamkakamiza, nagonanso komweko.

8. Nalawirira mamawa tsiku lacisanu kuti amuke, koma atate wa mkaziyo anati, Ulimbitse mtima wako, nulindire lipendeke dzuwa; nadya iwo onse awiri.

9. Pamenepo munthuyo ananyamuka kucoka, iye ndi mkazi wace wamng'ono ndi mnyamata wace; koma mpongozi wace, atate wa mkaziyo, ananena naye, Tapenya, lapendeka dzuwa, ugone kuno usiku; tapenya lapendekatu dzuwa, ugone kuno, nusekerere mtima wako; nimulawire mamawa kumka ulendo wanu kwanu.

10. Koma munthuyo anakana kugonako usiku, nanyamuka, nacoka, nadza pandunji pa Yebusi (ndiwo Yerusalemu); ndi pamodzi naye panali aburu awiri omangirira mbereko; anali nayenso mkazi wace wamng'ono.

11. Pofika iwo pa Yebusi linalimkulowa dzuwa, ndi mnyamata anati kwa mbuye wace, Tiyeni, tipambukire mudzi uwu wa Ayebusi ndi kugona pomwepa.

12. Koma mbuye wace ananena naye, Tisapambukire mudzi wacilendo, wosati wa ana a lsrayeli, koma tipitirire kumka ku Gibeya,

13. Nati kwa mnyamata wace, Tiyeni, tiyandikire kwinako: tigone m'Gibeya, kapena m'Rama.

14. Napitiriraiwo, nayenda, ndi dzuwa linawalowera pafupi pa Gibeya, ndiwo wa Benjamini.

15. Napambukirako, kuti alowe nagone ku Gibeya; nalowa iye, nakhala pansi m'khwalala la mudziwo, pakuti panalibe wina wowalandira m'nyumba agonemo, wakuwapatsa pogona.

16. Ndipo taonani, munthu nkhalamba anacokera ku nchito yace kumunda madzulo; munthuyu ndiye wa ku mapiri a Efraimu, nagonera ku Gibeya; kuma anthu pamenepo ndiwo Abenjamini.

17. Pamene anakweza maso ace anaona munthu wa pa ulendoyo m'khwalala la mudzi; ndi nkhalambayo inati, Umuka kuti? ufumira kuti?

18. Ndipo ananena nayo, Tirikucokera ku BetelehemuYuda, kumka ku mbali za mapiri a Efraimu, ndiko ndifumira ine; koma ndidamuka ku Betelehemu-Yuda; ndipo tsopano ndiri kumuka ku nyumba ya Yehova; koma palibe munthu wondipatsa nyumba.

Oweruza 19