Oweruza 16:11-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Nanena naye, Akandimangitsa nazo zingwe zatsopano, zosagwira nazo nchito pamenepo ndidzakhala: wofoka wakunga munthu wina.

12. Ndipo Delila anatenga nsinga zatsopano, nammanga nazo, nanena naye, Atilisti akugwera, Samsoni. Ndi omlalira analikulinda m'cipinda ca m'kati. Koma anazidula pa manja ace ngati thonje.

13. Pamenepo Delila anati kwa Samsoni, Mpaka tsopano wandipusitsa, ndi kundiuza mabodza; undiuze cimene angakumange naco. Nanena naye, Ukaomba njombi zisanu ndi ziwiri za pamutu panga mwa thonje loyala ndiko.

14. Ndipo anacimanga ndi phanga, nati kwa iye, Akugwera Afilisti, Samsoni; nagalamuka iye patulo tace, nazula phanga la pamtanda, ndi thonje loyala lomwe.

15. Pamenepo ananena naye, Ukati bwanji, Ndikukonda, osamvana nane mtima wako? wandipusitsa katatu tsopano, osandiuza umo mucokera mphamvu yako yaikuru,

16. Ndipo kunali, popeza anamuumiriza masiku onse ndi mau ace, oamkakamiza, moyo wace unabvutika nkufuna kufa.

17. Pomwepo anamfotokozera mtima wace wonse, nanena naye, Pamutu panga sipanapite lumo, pakuti ndine Mnaziri wa Mulungu ciyambire mimba ya mai wanga; akandimeta, mphamvu yanga idzandicokera, ndidzakhala wofoka wakunga munthu wina ali yense.

18. Ndipo pamene Delila anaona kuti adamfotokozera mtima wace wonse, anatuma naitana akalonga a Afilisti, ndi kuti, Kwerani nthawi yino, pakuti wandifotokozera za mtima wace wonse. Nakwera akalonga a Afilisti nadza kwa iye nabwera nazo ndalamazo m'dzanja lao.

19. Pamenepo anamgonetsa pa mabondo ace, naitana munthu, nameta njombi zace zisanu ndi ziwiri; nayamba kumzunza, nimcokera mphamvu yaceo

20. Ndipo anati, Afilisti akugwera, Samsoni. Nagalamuka iye m'tulo tace, nati, Ndizituruka ngati nthawi zina, ndi kudzitakasika. Koma sanadziwa kuti Yehova adamcokera.

21. Pamenepo Afilisti anamgwira, namkolowola maso, natsika naye ku Gaza, nammanga ndi maunyolo amkuwa; namperetsa m'kaidi.

22. Koma atammeta tsitsi la pamutu pace linayamba kumeranso.

23. Ndipo anasonkhana akalonga a Afilisti kuperekera Dagoni mulungu wao nsembe yaikuru, ndi kusekerera; pakuti anati, Mulungu wathu wapereka Samsoni mdani wathu m'dzanja lathu.

24. Ndipo pakumuona anthu analemekeza mulungu wao, pakuti anati, Mulungu wathu wapereka m'dzanja lathu mdani wathu, ndiye wakupasula dziko lathu, amene anatiphera ambiri.

25. Ndipo kunali, pakukondwera mitima yao, anati, Kaitaneni Samsoni, atisewerere. Naitana Samsoni m'kaidi; nasewera iye pamaso pao; ndipo anamuika iye pakati pa mizati.

26. Ndipo Samsoni anati kwa mnyamata womgwira dzanja, Ndileke, ndikhudze mizati imene nyumba ikhazikikapo, kuti nditsamirepo.

27. Koma nyumbayi inadzala ndi amuna ndi akazi; ndi akalonga onse a Afilisti anali momwemo ndi patsindwi panali amuna ndi akazi ngati zikwi zitatu akuyang'ana pakusewera Samsoni.

28. Pamenepo Samsoni anaitana kwa Yehova, nati, Yehova, Mulungu, dikupempha mundikumbukile, ndikupemphani, ndi kundilimbitsa, ndikupemphani, nthawi yino yokha, Mulungu, kuti ndidzilipsiriretu tsopano apa Afilisti, cifukwa ca maso anga awiri.

29. Ndipo Samsoni anagwira mizati iwiri ya pakati imene nyumba inakhazikikapo, natsamirapo wina ndi dzanja lamanja, ndi unzace ndi dzanja lamanzere.

Oweruza 16