1. Ndipo Iye analowa m'ngalawa, naoloka, nadza kumudzi kwao.
2. Ndipo onani, anabwera naye kwa Iye munthu wamanjenje, wakugona pachika: ndipo Yesu pakuona cikhulupiriro cao, anati kwa wodwalayo, Limba mtima, mwana, macimo ako akhululukidwa.
3. Ndipo onani, ena a alembi ananena mumtima mwao, Uyu acitira Mulungu mwano.
4. Ndipo Yesu, pozindikira maganizo ao, anati, Cifukwa canji mulinkuganizira zoipam'mitimayanu?
5. pakuti capafupi nciti, kunena, Macimo ako akhululukidwa; kapena kunena, Tanyamuka nuyende?
6. Koma kuti mudziwe kuti ali nazo mphamvu Mwana wa munthu pansi pano za kukhululukira macimo (pomwepo ananena kwa wodwalayo), Tanyamuka, nutenge chika lako, numuke kunyumba kwako.
7. Ndipo ananyamuka, napita ku nyumba kwace.
8. Ndipo m'mene anthu a makamu anaciona, anaopa, nalemekeza Mulungu, wakupatsa anthu mphamvu yotere.
9. Ndipo Yesu popita, kucokera kumeneko, anaona munthu, dzina lace Mateyu, alinkukhala polandirira msonkho, nanena kwa iye, Nditsate Ine. Ndipo iye anauka, namtsata.
10. Ndipo panali pamene Iye analinkukhala pacakudya m'nyumba, onani, amisonkho ndi ocimwa ambiri anadza nakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ace.
11. Ndipo Afarisi, pakuona ici, ananena kwa ophunzira ace, Cifukwa ninji Mphunzitsi wanu alinkudya pamodzi ndi amisonkho ndi ocimwa?
12. Ndipo m'mene Yesu anamva anati, Olimba safuna sing'anga ai, koma odwala.
13. Koma mukani muphunzire nciani ici:Ndifuna cifundo, si nsembe ai; pakuti sindinadza kudzaitana olungama, koma ocimwa.
14. Pomwepo anadza kwa Iye ophunzira ace a Yohane, nati, Cifukwa ninji ife ndi Afarisi tisala kudya kawiri kawiri, koma ophunzira anu sasala?