15. Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zobvala zankhosa, koma m'kati mwao ali afisi alusa.
16. Mudzawazindikira ndi zipatso zao. Kodi achera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula?
17. Comweco mtengo wabwino uli wonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuci upatsa zipatso zoipa,
18. Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuci kupatsa zipatso zokoma.
19. Mtengo uli wonse wosapatsa cipatso cokoma, audula, nautaya kumoto.
20. Inde comweco pa zipatso zao mudzawazindikira iwo.
21. Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakucitayo cifuniro ca Atate wanga wa Kumwamba.
22. Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mau m'dzina lanu, ndi m'dzina lanunso kuturutsa mizimu yoipa, ndi kucita m'dzina lanunso zamphamvu zambiri?
23. Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziwani inu nthawi zonse; cokani kwa Ine, inu akucita kusayeruzika.
24. Cifukwa cimeneci yense amene akamva mau anga amenewa, ndi kuwacita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wocenjera, amene anamanga nyumba yace pathanthwe;
25. ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; koma siinagwa; cifukwa inakhazikika pathanthwepo.
26. Ndipo yense akamva mau anga amenewa, ndi kusawacita, adzafanizidwa ndi munthu wopusa, yemwe anamanga nyumba yace pamcenga;
27. ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwace kunali kwakukuru.
28. Ndipo panakhala pamene Yesu anatha mau amenewa, makamu a anthu anazizwa ndi ciphunzitso cace:
29. pakuti anawaphunzitsa monga mwini mphamvu, wosanga alembiao.