Mateyu 25:19-39 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo Itapita nthawi yaikuru, anabwera mbuye wa akapolo awo, nawerengera nao pamodzi.

20. Ndipo uyo amene adalandira ndalama za matalente zisanu anadza, ali nazo ndalama zina zisanu, nanena, Mbuye, munandipatsa ndalama za matalente, zisanu, onani ndapindulapo ndalama zisanu zina.

21. Mbuye wace anati kwa iye, Cabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; Iowa iwe m'cikondwero ca mbuye wako.

22. Ndipo wa ndalama ziwiriyo anadzanso, nati, Mbuye, munandipatsa ine ndalama ziwiri; onani, ndapindulapo ndalama zina ziwiri.

23. Mbuye wace anati kwa iye, Cabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; Iowa iwe m'cikondwero ca mbuye wako.

24. Ndipo uyonso amene analandira ndalama imodzi, anadza, nati, Mbuye, ndinakudziwani inu kuti ndinu munthu wouma mtima, wakututa kumene simunafesa, ndi wakusonkhanitsa kumene simunawaza;

25. ndinaopa ine, ndinapita, ndinabisa pansi ndalama yanu: onani, siyi yanu.

26. Koma mbuye wace anayankha, nati kwa iye, Kapolo iwe woipa ndi waulesi, unadziwa kuti ndimatuta kumene sindinafesa, ndi kusonkhanitsa kumene sindinawaza;

27. cifukwa cace ukadapereka ndalama zanga kwa okongola ndalama, ndipo ine pobwera ndikadatenga zanga ndi phindu lace.

28. Cifukwa cace cotsani kwa iye ndalamayo, muipatse kwa amene ali nazo ndalama khumi.

29. Pakuti kwa yense amene ali nazo, kudzapatsidwa, ndipo iye adzakhala nazo zocuruka: koma kwa iye amene alibe, kudzacotsedwa, cingakhale cimene anali naco.

30. Ndipo ponyani kapoloyo wopanda pace ku mdima wakunja; kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.

31. Koma pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wace, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo Iye adzakhala pa cimpando ca kuwala kwace:

32. ndipo adzasonkhanidwa pamaso pace anthu a mitundu yonse; ndipo Iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzace, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi;

33. nadzakhalitsa nkhosa ku dzanja lace lamanja, koma mbuzi kulamanzere.

34. Pomwepo Mfumuyo idzanena kwa iwo a ku dzanja lace lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa cikhazikiro cace ca dziko lapansi:

35. pakuti ndinali ndi njala, ndipo munandipatsa Ine kudya; ndinali ndi ludzu, ndipo munandimwetsa Ine; ndinali mlendo, ndipo munacereza Ine;

36. wamarisece Ine, ndipo munandibveka; ndinadwala, ndipo munadza kuceza ndi Ine; ndinali m'nyumba yandende, ndipo munadza kwa Ine.

37. Pomwepo olungama adzamyankha Iye kuti, Ambuye, tinakuonani Inu liti wanjala, ndi kukudyetsani? kapena waludzu, ndi kukumwetsani?

38. Ndipo tinaona Inu liti mlendo, ndi kukucerezani? kapena wamarisece, ndi kukubvekani?

39. Ndipo tinakuonani Inu liti wodwala, kapena m'nyumba yandende, ndipo tinadza kwa Inu?

Mateyu 25