Ndipo uyo amene adalandira ndalama za matalente zisanu anadza, ali nazo ndalama zina zisanu, nanena, Mbuye, munandipatsa ndalama za matalente, zisanu, onani ndapindulapo ndalama zisanu zina.