11. Koma pambuyo pace anadzanso anamwali enawo, nati, Mbuye, Mbuye, mutitsegulire ife.
12. Koma iye anayankha nati, Indetu ndinena kwa inu, sindikudziwani.
13. Cifukwa cace dikirani, pakuti simudziwa tsiku lace, kapena nthawi yace.
14. Pakuti monga munthu, wakunka ulendo, aitana akapolo ace, napereka kwa iwo cuma cace.
15. Ndipo mmodzi anampatsa ndalama za matalente zisanu, ndi wina ziwiri, ndi wina imodzi; kwa iwo onse monga nzeru zao; namuka iye.
16. Pomwepo uyo amene analandira ndalama zisanu, anapita kugula nazo malonda, napindulapo ndalama zina zisanu.
17. Cimodzimodzinso uyo wa ziwirizo, anapindulapo zina ziwiri.
18. Koma uyo amene analandira imodziyo anamuka, nakumba pansi, naibisa ndalama ya mbuye wace.
19. Ndipo Itapita nthawi yaikuru, anabwera mbuye wa akapolo awo, nawerengera nao pamodzi.
20. Ndipo uyo amene adalandira ndalama za matalente zisanu anadza, ali nazo ndalama zina zisanu, nanena, Mbuye, munandipatsa ndalama za matalente, zisanu, onani ndapindulapo ndalama zisanu zina.
21. Mbuye wace anati kwa iye, Cabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; Iowa iwe m'cikondwero ca mbuye wako.
22. Ndipo wa ndalama ziwiriyo anadzanso, nati, Mbuye, munandipatsa ine ndalama ziwiri; onani, ndapindulapo ndalama zina ziwiri.
23. Mbuye wace anati kwa iye, Cabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; Iowa iwe m'cikondwero ca mbuye wako.
24. Ndipo uyonso amene analandira ndalama imodzi, anadza, nati, Mbuye, ndinakudziwani inu kuti ndinu munthu wouma mtima, wakututa kumene simunafesa, ndi wakusonkhanitsa kumene simunawaza;
25. ndinaopa ine, ndinapita, ndinabisa pansi ndalama yanu: onani, siyi yanu.
26. Koma mbuye wace anayankha, nati kwa iye, Kapolo iwe woipa ndi waulesi, unadziwa kuti ndimatuta kumene sindinafesa, ndi kusonkhanitsa kumene sindinawaza;
27. cifukwa cace ukadapereka ndalama zanga kwa okongola ndalama, ndipo ine pobwera ndikadatenga zanga ndi phindu lace.
28. Cifukwa cace cotsani kwa iye ndalamayo, muipatse kwa amene ali nazo ndalama khumi.