Mateyu 23:2-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. nanena, Alembi ndi Afarisi akhala pa mpando wa Mose;

3. cifukwa cace zinthu ziri zonse zimene iwo akauza inu, citani nimusunge; koma musatsanza nchito zao; pakuti iwo amalankhula, komasamacita.

4. Inde, amanga akatundu olemera ndi osautsa ponyamula, nawasenza pa mapewa a anthu; koma iwo eni okha safuna kuwasuntha amenewo ndi cala cao.

5. Koma amacita nchito zao zonse kuti aonekere kwa anthu; pakuti akulitsa citando cace ca njirisi zao, nakulitsa mphonje,

6. nakonda malo a ulemu pamapwando, ndi mipando ya ulemu m'masunagoge,

7. ndi kulankhulidwa m'misika, ndi kuchedwa ndi anthu, Rabi.

8. Koma inu musachedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale.

9. Ndipo inu musachule wina atate wanu pansi pano, pakuti alipo mmodzi ndiye Atate wanu wa Kumwamba.

10. Ndipo musachedwa atsogoleri, pakuti alipo mmodzi Mtsogoleri wanu, ndiye Kristu.

11. Koma wamkuru wopambana wa inu adzakhala mtumiki wanu.

12. Ndipo amene ali yense akadzikuza yekha adzacepetsedwa; koma amene adzicepetsa mwini yekha adzakulitsidwa.

13. Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, Ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo. [

14. ]

15. Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mupitapita kunyanja ndi kumtunda kuyesa munthu mmodzi mtembenuki; ndipo m'mene akhala wotere, mumsandutsa mwana wa gehena woposa inu kawiri.

16. Tsoka inu, atsogoleri akhungu, amene munena, Amene ali yense akalumbira kuchula Kacisi, palibe kanthu; koma amene akalumbira kuchula golidi wa Kacisi, wadzimangirira.

17. Inu opusa, ndi akhungu: pakuti coposa nciti, golidi kodi, kapena Kacisi amene ayeretsa golidiyo?

18. Ndiponso, Amene ali yense akalumbira kuchula guwa la nsembe, palibe kanthu; koma amene akalumbira kuchula mtulo wa pamwamba pace wadzimangirira.

19. Inu akhungu, pakuti coposa nciti, mtulo kodi, kapena guwa la nsembe limene liyeretsa mtulowo?

Mateyu 23