12. Ndipo amene ali yense akadzikuza yekha adzacepetsedwa; koma amene adzicepetsa mwini yekha adzakulitsidwa.
13. Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, Ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo. [
14. ]
15. Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mupitapita kunyanja ndi kumtunda kuyesa munthu mmodzi mtembenuki; ndipo m'mene akhala wotere, mumsandutsa mwana wa gehena woposa inu kawiri.
16. Tsoka inu, atsogoleri akhungu, amene munena, Amene ali yense akalumbira kuchula Kacisi, palibe kanthu; koma amene akalumbira kuchula golidi wa Kacisi, wadzimangirira.
17. Inu opusa, ndi akhungu: pakuti coposa nciti, golidi kodi, kapena Kacisi amene ayeretsa golidiyo?
18. Ndiponso, Amene ali yense akalumbira kuchula guwa la nsembe, palibe kanthu; koma amene akalumbira kuchula mtulo wa pamwamba pace wadzimangirira.
19. Inu akhungu, pakuti coposa nciti, mtulo kodi, kapena guwa la nsembe limene liyeretsa mtulowo?
20. Cifukwa cace wakulumbira kuchula guwa la nsembe, alumbira limenelo ndi zonse za pamwamba pace.
21. Ndipo wakulumbira kuchula Kacisi, alumbira ameneyo ndi Iye wakukhala momwemo.
22. Ndipo wakulumbira kuchula Kumwamba, alumbira cimpando ca Mulungu, ndi Iye wakukhala pomwepo.
23. Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi katsabola, ndi la citowe, nimusiya zolemera za cilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kucitira cifundo, ndi cikhulupiriro; koma zijazo munayenera kuzicita, osasiya izi zomwe.
24. Atsogoleri akhungu inu, akukuntha udzudzu, koma ngamila mummeza.
25. Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mutsuka kunja kwace kwa cikho ndi mbale, koma m'katimo iwo adzala ndi kulanda ndi kusadziletsa.
26. Mfarisi iwe wakhungu, yambotsuka m'kati mwa cikho ndi mbale, kuti kunja kwace kukhalenso koyera.
27. Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mufanafana ndi manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwace, koma adzala m'katimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse.