21. ndipo alibe mizu mwa iye, koma akhala nthawi yaing'ono; ndipo pakudza nsautso kapena zunzo cifukwa ca mau, iye akhumudwa pomwepo.
22. Ndipo iye amene afesedwa kuminga, uyu ndiye wakumva mau; ndipo kulabadira kwa dziko lapansi, ndi cinyengo ca cuma citsamwitsa mau, ndipo akhala wopanda cipatso.
23. Ndipo iye amene afesedwa pa nthaka yabwino, uyu ndiye wakumva mau nawadziwitsa; amene abaladi zipatso, nazifitsa, ena za makumi khumi, ena za makumi asanu ndi limodzi, ena za makumi atatu.
24. Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, amene anafesa mbeu zabwino m'munda mwace;
25. koma m'mene anthu analinkugona, mdani wace anadza, nafesa namsongole pakati pa tirigu, nacokapo.
26. Koma pamene mmera unakula, nubala cipatso, pomwepo anaonekeranso namsongole.
27. Ndipo anyamata ace a mwini nyumbayo anadza, nati kwa iye, Mbuye, kodi simunafesa mbeu zabwino m'munda mwanu? nanga wacokera kuti namsongoleyo?
28. Ndipo iye ananena kwa iwo, Munthu mdani wanga wacicita ici. Ndipo anyamata anati kwa iye, Kodi mufuna tsopano kuti timuke, tikamsonkhanitse uyo pamodzi?
29. Koma iye anati, lai, kuti kapena m'mene mukasonkhanitsa namsongoleyo, mungazulenso tirigu pamodzi naye.
30. Kazilekeni zonse ziwiri, zikulire pamodzi kufikira pakututa; ndimo m'nyengo yakututa ndidzauza akututawo, Muyambe kusonkhanitsa namsongole, mummange uyu mitolo kukamtentha, koma musonkhanitse tirigu m'nkhokwe yanga.
31. Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi kambeu kampiru, kamene anakatenga munthu, nakafesa pamunda pace;
32. kamene kakhaladi kakang'ono koposa mbeu zonse, koma katakula, kali kakakuru kuposa zitsambazonse, nukhala mtengo, kotero kuti mbalame za mlengalenga zimadza, nizibindikira mu nthambi zace.
33. Fanizo lina ananena kwa iwo; Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi cotupitsa mikate, cimene mkazi anacitenga, nacibisa m'miyeso itatu ya ufa, kufikira wonse unatupa.