Mateyu 12:31-48 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Cifukwa cace ndinena kwa inu, Macimo onse, ndi zonena zonse zamwano, zidzakhululukidwa kwa anthu; koma camwano ca pa Mzimu Woyera sicidzakhululukidwa.

32. Ndipo amene ali yense anganenere Mwana wa munthu zoipa, adzakhululukidwa; koma amene ali yense anganenere Mzimu Woyera zoipa sadzakhululukidwa nthawi yino kapena irinkudzayo.

33. Ukakoma mtengo, cipatso cace comwe cikoma; ukaipa mtengo, cipatso cace comwe ciipa; pakuti ndi cipatso cace mtengo udziwika.

34. Akubadwa inu a njoka, mungathe bwanji kulankhula zabwino, inu akukhala oipa? pakuti m'kamwa mungolankhula mwa kusefuka kwace kwa mtima.

35. Munthu wabwino aturutsa zabwino m'cuma cace cabwino, ndi munthu woipa aturutsa zoipa m'cuma cace coipa.

36. Ndipo ndinena kwa inu, kuti mau onse opanda pace, amene anthu adzalankhula, adzawawerengera mlandu wace tsiku la kuweruza.

37. Pakuti udzayesedwa wolungama ndi mau ako, ndipo ndi mau ako omwe udzatsutsidwa.

38. Pomwepo alembi ndi Afarisi ena anayankha Iye nati, Mphunzitsi, tifuna kuona cizindikiro ca Inu.

39. Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Akubadwa oipa acigololo afunafuna cizindikiro; ndipo sicidzapatsidwa kwa iwo cizindikiro, komatu cizindikiro ca Yona mneneri;

40. pakuti monga Yona anali m'mimba mwa cinsomba masiku atatu ndi usiku wace, comweco Mwana wa munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wace.

41. 1 Anthu a ku Nineve adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; cifukwa 2 iwo anatembenuka mtima ndi kulalikira kwace kwa Yona; ndipo onani, wakuposa Y ona ali pano.

42. 3 Mfumu yaikazi ya kumwera adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; cifukwa iye anacokera ku mathero a dziko lapansi kudzamva nzeru ya Solomo; ndipo onani, wakuposa Solomo ali pano.

43. Koma mzimu wonyansa, utaturuka mwa munthu, umapitirira malo opanda madzi kufunafuna mpumulo, osaupeza.

44. Pomwepo unena, ndidzabwerera kunka kunyumba kwanga, konkuja ndinaturukako; ndipo pakufikako uipeza yopanda wokhalamo, yosesedwa ndi yokonzedwa.

45. Pomwepo upita, nutenga pamodzi ndi uwu mizimu yina inzace isanu ndi iwiri yoipa yoposa mwini yekhayo, ndipo ilowa, nikhalamo. Ndipo 4 matsirizidwe ace a munthu uyo akhala oipa oposa mayambidwe ace. Kotero kudzakhalanso kwa obadwa oipa amakono.

46. Pamene Iye anali cilankhulire ndi makamu, onani, amace ndi 5 abale ace anaima panja, nafuna kulankhula naye.

47. Ndipo munthu anati kwa Iye, Onani, amai wanu ndi abale anu aima pabwalo, nafuna kulankhula nanu.

48. Koma Iye anayankha, nati kwa iye wonenayo, Amai wanga ndani? ndi abale anga ndi ayani?

Mateyu 12