Danieli 3:13-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Pamenepo Nebukadinezara, mumkwiyo ndi m'ukali wace, anawauza abwere nao Sadrake, Mesake, ndi Abedinego. Ndipo anabwera nao amunawa kwa mfumu.

14. Nebukadinezara anayankha, nati kwa iwo, Kodi mutero dala, Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, kusatumikira milungu yanga, ndi kusalambira fano lagolidi ndinaliimikalo?

15. Mukabvomereza tsono, pakumva mau a lipenga, citoliro, zeze, sansi, cisakasa, ndi ngoli, ndi zoyimbitsa ziri zonse, kugwadira ndi kulambira fano ndinalipanga, cabwino; koma mukapanda kulambira, mudzaponyedwa nthawi yomweyi m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto; ndipo mulungu amene adzakulanditsani m'manja mwanga ndani?

16. Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, anayankha, nati kwa mfumu Nebukadinezara, Sikufunika kuti tikuyankheni pa mlandu uwu.

17. Taonani, Mulungu wathu amene timtumikira akhoza kutilanditsa m'ng'anjo yotentha yamoto, nadzatilanditsa m'dzanja lanu, mfumu.

18. Koma akapanda kutero, dziwani, mfumu, kuti sitidzatumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolidi mudaliimikalo.

19. Pamenepo Nebukadinezara anadzazidwa ndi ukali, ndi maonekedwe a nkhope yace anasandulikira Sadrake, Mesake, ndi Abedinego; anayankha, nati asonkheze ng'anjo kasanu ndi kawiri koposa umo amasonkhezera.

20. Nauza amuna ena amphamvu a m'khamu lace la nkhondo amange Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, ndi kuwaponya m'ng'anjo yotentha yamoto.

21. Pamenepo amuna awa anamangidwa ali cibvalire zopfunda zao, maraya ao, ndi nduwira zao, ndi zobvala zao zina; naponyedwa m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto.

22. Motero, popeza mau a mfumu anafulumiza, ndi ng'anjo inatentha koposa, lawi la moto linapha iwo aja ananyamula Sadrake, Mesake, ndi Abedinego.

23. Ndipo amuna atatu awa, Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, anagwa pansi omangidwa m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto.

24. Pamenepo mfumu Nebukadinezara anadabwa, nauka msanga, nanena nati kwa mandoda ace, Kodi sitinaponya amuna atatu omangidwa m'kati mwa moto? Anayankha nati kwa mfumu, Inde mfumu.

25. Anayankha, nati, Taonani, ndirikuona amuna anai omasuka, alikuyenda m'kati mwa moto; ndipo alibe kuphwetekwa, ndi maonekedwe a wacinai akunga mwana wa milungu.

26. Pamenepo Nebukadinezara anayandikira pa khomo la ng'anjo yotentha yamoto, analankhula, nati, Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, inu atumiki a Mulungu Wam'mwambamwamba, turukani, idzani kuno. Pamenepo Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, anaturuka m'kati mwa moto.

27. Ndipo akalonga, akazembe, ndi ziwanga, ndi mandoda a mfumu, atasonkhana, anaona amuna awa, kuti moto unalibe mphamvu pa matupi ao, losawauka tsitsi la pamutu pao, ndi zopfunda zao zosasandulika, pfungo lomwe lamoto losawaomba.

28. Nebukadinezara ananena, nati, Alemekezedwe Mulungu wa Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, amene anatuma mthenga wace, napulumutsa atumiki ace omkhulupirira Iye, nasanduliza mau a ine mfumu, napereka matupi ao kuti asatumikire kapena kulambira mulungu wina yense, koma Mulungu wao wao.

Danieli 3