13. Momwemo anacita ogwira nchito, nikula nchito mwa dzanja lao, nakhazikitsa iwo nyumba ya Mulungu monga mwa maonekedwe ace, nailimbitsa.
14. Ndipo ataitsiriza, anabwera nazo ndalama zotsala kwa mfumu ndi Yehoyada, napanga nazo zipangizo za nyumba ya Yehova, zipangizo za kutumikira nazo, ndi kupereka nsembe nazo, ndi zipande, ndi zipangizo za golidi ndi siliva. Ndipo anapereka kosalekeza nsembe zopsereza m'nyumba ya Yehova masiku onse a Yehoyada.
15. Koma Yehoyada anakalamba, nacuruka masiku, namwalira iye; ndiye wa zaka zana limodzi mphambu makumi atatu pamene anamwalira.
16. Ndipo anamuika m'mudzi wa Davide, pakati pa mafumu; pakuti anacita zabwino m'Israyeli, ndi kwa Mulungu, ndi ku nyumba yace.
17. Atamwalira Yehoyada tsono, akalonga a Yuda anadza, nalambira mfumu. Ndipo mfumu inawamvera.
18. Ndipo anasiya nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo ao, natumikira zifanizo, ndi mafano; ndipo mkwiyo unawagwera Yuda ndi Yerusalemu, cifukwa ca kuparamula kwao kumene.
19. Koma Iye anawatumira aneneri kuwabwezeranso kwa Yehova, ndiwo anawacitira umboni; koma sanawamvera.
20. Ndipo mzimu wa Mulungu unabvala Zekariya mwana wa Yehoyada wansembe, naima iye kumtunda kwa anthu, nanena nao, Atero Mulungu, Mulakwiranji malamulo a Yehova kuli kosalemerera nako? Popeza mwasiya Yehova, Iye wasiyanso inu.
21. Koma anampangira ciwembu, namponya miyala, mwa lamulo la mfumu m'bwalo la nyumba ya Yehova.
22. Motero mfumu Yoasi sanakumbukila zokoma anamcitirazi Yehoyada atate wace, koma anapha mwana wace; ndiye pomwalira anati, Yehova acipenye, nacifunse.
23. Ndipo kunacitika, podzanso nyengoyi khamu la nkhondo la Aaramu linamkwerera, nafika iwo ku Yuda ndi Yerusalemu, naononga mwa anthu akalonga onse a anthu, natumiza zofunkha zao zonse kwa mfumu ya ku Damasiko.
24. Pakuti khamu la nkhondo la Aaramu linadza la anthu owerengeka; ndipo Yehova anapereka khamu lalikuru m'dzanja lao; popeza adasiya Yehova Mulungu wa makolo ao. Motero anacitira Yoasi zomlanga.
25. Ndipo atamcokera (popeza anamsiya wodwala nthenda zazikuru), anyamata ace anamcitira ciwembu, cifukwa ca mwazi wa ana a Yehoyada wansembe, namupha pakama pace, namwalira iye; ndipo anamuika m'mudzi wa Davide, koma osamuika m'manda a mafumu.
26. Omcitira ciwembu ndi awa: Zabadi, mwana wa Simeati wamkazi M-amoni; ndi Yozabadi, mwana wa Simiriti wamkazi Mmoabu.
27. Za ana ace tsono, ndi katundu wamkuru anamsenza, ndi kumanganso kwa nyumba ya Mulungu, taonani, zilembedwa m'buku lomasulira la mafumu. Ndipo Amaziya mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.