1 Mbiri 9:18-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. amene adadikira pa cipata ca mfumu kum'mawa mpaka pomwepo, ndiwo odikira pakhomo a tsasa la ana a Levi.

19. Ndipo Salumu mwana wa Kore, mwana wa Ebiasafu; mwana wa Kora, ndi abale ace a nyumba ya atate wace; Akora anayang'anira nchito ya utumiki, osunga zipata za kacisi monga makolo ao; anakhala m'cigono ca Yehova osunga polowera;

20. ndi a Pinehasi mwana wa Eleazara anali mtsogoleri wao kale, ndipo Yehova anali naye.

21. Zekariya mwana wa Meselemiya anali wodikira pakhomo pa cihema cokomanako.

22. Iwo onse osankhidwa akhale odikira kuzipata ndiwo mazana awiri mphambu khumi ndi awiri. Iwo anawerengedwa monga mwa cibadwidwe cao, m'midzi mwao, amene Davide ndi Samueli mlauli anawaika m'udindo wao.

23. Momwemo iwo ndi ana ao anayang'anira zipata za ku nyumba ya Yehova, ndiyo nyumba ya kacisi, m'udikiro wao.

24. Pa mbali zinai panali odikira kum'mawa, kumadzulo, kumpoto, ndi kumwela.

25. Ndi abale ao m'midzi mwao akafikafika, atapita masiku asanu ndi awiri masabata onse, kuti akhale nao;

26. pakuti odikira anai akuru, ndiwo Alevi, anali m'udindo wao, nayang'anira zipinda ndi mosungiramo cuma m'nyumba ya Mulungu.

27. Ndipo amagona usiku m'zipinda zozinga nyumba ya Mulungu, popeza udikiro wace ndi wao; kuitsegula m'mawa ndi m'mawa ndi kwaonso.

28. Ndi ena a iwo anayang'anira zipangizo za utumikiwo, pakuti analowa nazo ataziwerenga, naturuka nazo ataziwerenga.

29. Ndi ena a iwo anaikidwa ayang'anire zipangizo ziti zonse, ndi zipangizo zonse za malo opatulika, ndi ufa wosalala, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi libano, ndi zonunkhira.

30. Ndi ana ena a, ansembe anasanganiza cisanganizo ca zonunkhira,

31. Ndi Matitiya wina wa Alevi, ndiye mwana woyamba wa Salumu Mkora, anaikidwa ayang'anire zokazingidwa m'ziwaya.

32. Ndi ena a abale ao, a ana a Akohati, anayang'anira mkate woonekera, kuukonza masabata onse.

33. Ndipo awa ndi oyimba akuru a nyumba za makolo a Alevi, okhala m'zipinda, omasuka ku nchito zina; pakuti anali nayo nchito yao usana ndi usiku.

34. Awa ndi akuru a nyumba za makolo a Alevi mwa mibadwo yao, ndiwo akuru; anakhala ku Yerusalemu awa.

35. Ndipo m'Gibeoni munakhala atate wa Gibeoni Yeieli, dzina la mkazi wace ndiye Maaka;

36. ndi mwana wace woyamba ndiye Abidoni, opandana naye ndi Zuri, ndi Kisi, ndi Baala, ndi Neri, ndi Nadabu,

37. ndi Gedoro, ndi Ahiya, ndi Zekariya, ndi Mikiloti.

38. Ndi Mikiloti anabala Simeamu. Ndipo iwonso anakhala pamodzi ndi abale ao m'Yerusalemu, pandunji pa abale ao.

1 Mbiri 9