1. Ndipo kunali, utatha kuoloka Yordano mtundu wonse, Yehova ananena ndi Yoswa, nati,
2. Mudzitengere mwa anthu, amuna khumi ndi awiri, pfuko limodzi mwamuna mmodzi;
3. ndipo muwalamulire iwo ndi kuti, Mudzitengere pano pakati pa Yordano, poimapo mapazi a ansembe, miyala khumi ndi iwiri, ndi kuoloka nayo, ndi kulika m'mogona m'mene mugonamo usiku uno.
4. Pamenepo Yoswa anaitana amuna khumi ndi awiriwo amene anawaikiratu mwa ana a Israyeli, pfuko limodzi mwamuna mmodzi;
5. nanena nao Yoswa, Olokani, kutsogolera likasa la Yehova Mulungu wanu pakati pa Yordano, nimudzisenzere yense mwala paphewa pace, monga mwa kuwerenga kwa mapfuko a ana a Israyeli;
6. kuti ici cikhale cizindikilo pakati pa inu. Akakufunsani ana anu m'tsogolomo, ndi kuti, Miyala iyi nja ciani ndi inu?
7. munene nao, Cifukwa madzi a Yordano anadulidwa patsogolo pa likasa la cipangano ca Yehova; muja lidaoloka Yordano, madzi a Yordano anadulidwa; ndipo miyala iyi idzakhala cikumbutso ca ana a Israyeli cikhalire.