Yohane 4:44-54 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

44. Pakuti Yesu mwini anacita umboni kuti, Mneneri alibe ulemu m'dziko la kwao.

45. Cifukwa cace pamene anadza ku Galileya, Agalileva anamlandira iye, atakaona zonse zimene anazicita m'Yerusalemu paphwando; pakuti iwonso ananka kuphwando.

46. Cifukwa cace Yesu anadzanso ku Kana wa m'Galileya, kumene anasandutsa madzi vinyo. Ndipo kunalimkulu wina wa mfumu, mwana wace anadwala m'Kapernao.

47. Iyeyu, pamene anamva kuti Yesu wacokera ku Yudeya nafika ku Galileya, ananka kwa iye, nampempha kuti atsike kukaciritsa mwana wace; pakuti anali pafupi imfa.

48. Pamenepo Yesu anati kwa iye, Ngati simuona zizindikilo ndi zozizwa, simudzakhulupira.

49. Mkuluyo ananena kwa iye, Ambuye, tsikani asanafe mwana wanga.

50. Yesu ananena naye, Muka, mwana wako ali ndi moyo, Munthuyo anakhulupirira mau amene Yesu anatero naye, namuka.

51. Ndipo m'mene analikutsika, akapolo ace anakomana, naye, nanena, kuti, Mwana wanu ali ndi moyo.

52. Cifukwa cace anawafunsa ora lace anayamba kuciralo. Pamenepo anati kwa iye, kuti, Dzulo, ora lacisanu ndi ciwiri malungo anamsiya.

53. Cifukwa cace atateyo anadziwa kuti ndi ora lomwelo limene Yesu anati kwa iye, Mwana wako ali ndi moyo; ndipo anakhulupira iye yekha ndi a pa banja lace onse.

54. Ici ndi cizindikilo caciwiri Yesu anacita, ataeokera ku Yudeya, ndi kulowa m'Galileya.

Yohane 4