5. Ndipo kunatero, atatha masiku a madyererowa Yobu anatumiza mau, nawapatula, nauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, monga mwa kuwerenga kwa iwo onse; pakuti Yobu anati, Kapena anacimwa ana anga, nacitira Mulungu mwano m'mtima mwao. Anatero Yobu masiku onse.
6. Ndipo panali tsiku lakuti ana a Mulungu anadza kudzionetsa kwa Yehova, nadzanso Satana pakati pao.
7. Nati Yehova kwa Satana, Ufuma kuti? Nayankha Satana kwa Yehova, nati, Kupitapita m'dziko ndi kuyendayenda m'mwemo.
8. Ndipo Yehova anati kwa Satana, Kodi waonerera mtumiki wanga Yobu? pakuti palibe wina wonga iye m'dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.
9. Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Kodi Yobu aopa Mulungu pacabe?
10. Kodi simunamcinga iye ndi nyumba yace, ndi zace zonse, pomzinga ponse? nchito ya manja ace mwaidalitsa, ndi zoweta zace zacuruka m'dziko.
11. Koma mutambasule dzanja lanu ndi kumkhudzira zace zonse, ndipo adzakucitirani mwano pankhope panu.
12. Nati Yehova kwa Satana, Taona, zonse ali nazo zikhale m'dzanja mwako; pa iye pokha usatambasula dzanja lako. Naturuka Satana pamaso pa Yehova.
13. Tsono panali tsiku loti ana ace amuna ndi akazi analinkudya ndi kumwa vinyo m'nyumba ya mkuru wao;
14. nafika mthenga kwa Yobu, nati, Ng'ombe zinalikulima, ndi aburu akazi analikudya pambali pao;
15. koma anazigwera Aseba, nazitenga, nawapha anyamata ndi lupanga lakuthwa, ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.
16. Akali cilankhulire uyu, anadza winanso, nati, Wagwa moto wa Mulungu wocokera kumwamba, wapsereza nkhosa ndi anyamata, nuzinyeketsa; ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.
17. Akali cilankhulire uyu, anadza winanso, nati, Akasidi anadzigawa magulu atatu, nazigwera ngamila, nazitenga, nawapha anyamata ndi lupanga lakuthwa, ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.
18. Akali cilankhulire, anadza winanso, nati, Ana anu amuna ndi akazi analinkudya ndi kumwa vinyo m'nyumba ya mkuru wao;
19. ndipo taonani, inadza mphepo yaikuru yocokera kucipululu, niomba pa ngondya zonse zinai za nyumbayo, nigwa pa anyamatawo, nafa; ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.