20. Nati kwa Yeteri mwana wace woyamba, Tauka, nuwaphe. Koma mnyamatayo sanasolola lupanga lace; pakuti anaopa, pokhala anali mnyamata.
21. Pamenepo Zeba ndi Tsalimuna anati, Tauka iwe mwini nutigwere; pakuti monga munthu momwemo mphamvu yace. Ndipo Gideoni anauka nawapha Zeba ndi Tsalimuna, nalanda mphande zinali kukhosi kwa ngamila zao.
22. Pamenepo anthu a Israyeli anati kwa Gideoni, Mutilamulire ndi inu, ndi mwana wanu, ndi mdzukulu wanu, pakuti mwatipulumutsa m'dzanja la Amidyani.
23. Koma Gideoni ananena nao. Sindidzalamulira inu, ngakhale mwana wanga sadzalamulira inu; Yehova adzalamulira inu.
24. Gideoni anatinso kwa iwo, Mundilole ndipemphe kanthu kamodzi kwa inu, mundipatse ali yense mapelele mwa zofunkha zanu; pakuti anali nao mapelele agolidi, pokhala anali Aismayeli.
25. Ndipo anayankha, Kupereka tiwapereka; nayalapo cobvala, naponyamo yense mapelele a mwa zofunkha zao.
26. Ndipo kulemera kwace kwa mapelele agolidi adawapempha ndiko masekeli cikwi cimodzi ndi mazana asanu ndi awiri; osawerenga mphande, ndi zitunga ndi zobvala zacibakuwa za pa mafumu a ku Midyani, osawerenganso maunyolo okhala pa makosi a ngamila zao.
27. Ndipo Gideoni anawapanga fano, naliika m'mudzi mwace, ndiwo Ofira; ndi Israyeli yense analitsata kuligwadira pomwepo; ndipo linakhala kwa Gideoni ndi nyumba yace ngati msampha.
28. Motero anagonjetsa Amidyani pamaso pa ana a Israyeli, osaweramutsanso mitu yao iwowa. Ndipo dziko lidapumula zaka makumi anai m'masiku a Gideoni.
29. Ndipo Yerubaala, mwana wa Yoasi anamuka, nakhala, m'nyumba ya iye yekha.
30. Nakhala nao ana amuna makumi asanu ndi awiri Gideoni, anawabala ndi iye; popeza anali nao akazi ambiri.
31. Ndipo mkazi wace wamng'ono wokhala m'Sekemu, iyenso anambalira mwana wamwamuna; namucha dzina lace Abimeleki.
32. Ndipo Gideoni mwana wa Yoasi anafa atakalamba bwino, naikidwa m'manda a Yoasi atate wace, m'Ofira wa Aabiezeri.
33. Ndipo kunali, atafa Gideoni, ana a Israyeli anabwereranso nagwadira Abaala, nayesa Baala-beriti mulungu wao.
34. Ndi ana a Israyeli sanakumbukila Yehova Mulungu wao, amene anawapulumutsa m'dzanja la adani ao onse pozungulira ponse;
35. osacitira cifundo nyumba ya Yerubaala, ndiye Gideoni, monga mwa zokoma zonse iye anacitira Israyeli.