13. Pamenepo Gideoni mwana wa Yoasi anabwerera kunkhondo pokwerera pa Heresi.
14. Ndipo anagwira mnyamata wa anthu a ku Sukoti, nafunsira; ndipo anamsimbira akalonga a ku Sukoti, ndi akulu ace amuna makumi asanu ndi awiri kudza asanu ndi awiri.
15. Ndipo anafika kwa amuna a ku Sukoti, nati, Tapenyani Zeba ndi Tsalimuna amene munanditonza nao ndi kuti, Kodi manja a Zeba ndi Tsalimuna akhala m'dzanja lako, kuti tiwaninkhe mkate amuna ako akulema?
16. Ndipo anagwira akulu, a m'mudzi ndi minga ya kucipululu ndi mitungwi, nawalanga nazo amuna a ku Sukoti.
17. Ndipo anagamula nsanja ya Penueli, napha amuna a kumudzi.
18. Pamenepo anati kwa Zeba ndi Tsalimuna, Amunawo munawapha ku Tabori anali otani? Iwo nayankha, Monga iwe momwemo iwowa; yense wakunga mwana wa mfumu.
19. Ndipo anati, Ndiwo abale anga, ana a mai wanga. Pali Yehova mukadawasunga amoyo, sindikadakuphani.
20. Nati kwa Yeteri mwana wace woyamba, Tauka, nuwaphe. Koma mnyamatayo sanasolola lupanga lace; pakuti anaopa, pokhala anali mnyamata.
21. Pamenepo Zeba ndi Tsalimuna anati, Tauka iwe mwini nutigwere; pakuti monga munthu momwemo mphamvu yace. Ndipo Gideoni anauka nawapha Zeba ndi Tsalimuna, nalanda mphande zinali kukhosi kwa ngamila zao.
22. Pamenepo anthu a Israyeli anati kwa Gideoni, Mutilamulire ndi inu, ndi mwana wanu, ndi mdzukulu wanu, pakuti mwatipulumutsa m'dzanja la Amidyani.