7. Ndipo kunali, pamene ana a Israyeli anapfuula kwa Yehova cifukwa ca Midyani,
8. Yehova anatuma munthu mneneri kwa ana a Israyeli, nanena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Ine ndinakukwezani kucokera m'Aigupto, ndi kukuturutsani m'nyumba ya ukapolo;
9. ndipo ndinakulanditsani m'dzanja la Aaigupto, ndi m'dzanja la onse akupsinja inu, ndi kuwaingitsa pamaso panu, ndi kukupatsani dziko lao;
10. ndipo ndinati kwa inu, Ine ndine Yehova Mulungu wanu; musamaopa milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma simunamvera mau anga.
11. Pamenepo anadza mthenga wa Yehova, nakhala patsinde pa thundu wokhala m'Ofira, wa Yoasi M-abieziri; ndi mwana wace Gideoni analikuomba tirigu m'mopondera mphesa, awabisire Amidyani.
12. Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera, nati kwa iye, Yehova ali nawe, ngwazi iwe, wamphamvu iwe.
13. Ndipo Gideoni ananena naye, Mbuye wanga, ngati Yehova ali nafe catigwera ife bwanji conseci? ndipo ziti kuti zodabwiza zace zonse zimene makolo athu anatiwerengera, ndi kuti, Sanatikweza kodi Yehova kucokera m'Aigupto? Koma tsopano Yehova watitaya natipereka m'dzanja la Midyani.
14. Pamenepo Yehova anamtembenukira, nati, Muka nayo mphamvu yako iyi, nupulumutse Israyeli m'dzanja la Midyani, Sindinakutuma ndi Ine kodi?
15. Ndipo anati kwa iye, Ha! Mbuye, ndidzapulumutsa Israyeli ndi ciani? Taonani, banja langa liri loluluka m'Manase, ndipo ine ndine wamng'ono m'nyumba ya atate wanga.
16. Ndipo Yehova ananena naye, Popeza Ine ndidzakhala nawe udzakantha Amidyani ngati munthu mmodzi.
17. Ndipo anati kwa iye, Ngati mundikomera mtima mundionetse cizindikilo tsopano cakuti ndi Inu wakunena nane.
18. Musacoke pano, ndikupemphani, mpaka ndikudzerani ndi kuturutsa copereka canga ndi kuciika pamaso panu. Ndipo anati, Ndidzalinda mpaka ubwera.
19. Ndipo Gideoni analowa, nakonza kambuzi ndi mikate yopanda cotupitsa ya muyeso wa ufa; nyamayi anaiika m'licero, ndi msuzi anauthira mumbale, naturuka nazo kwa iye ali patsinde pa thundu, nazipereka.
20. Koma mthenga wa Mulungu ananena naye, Tenga nyamayi ndi mikate yopanda cotupitsa ndi kuziika pathanthwe pano ndi kutsanula msuzi. Ndipo anatero.
21. Pamenepo mthenga wa Yehova anatambasula nsonga ya ndodo inali m'dzanja lace, nakhudza nyamayi ndi mikate yopanda cotupitsa; ndipo unaturuka moto m'thanthwe nunyeketsa nyama ndi mikate yopanda cotupitsa; ndi mthenga wa Yehova anakanganuka pamaso pace.
22. Pamenepo Gideoni anaona kuti ndiye mthenga wa Yehova, nati Gideoni, Tsoka ine, Yehova Mulungu! popeza ndaona mthenga wa Yehova maso ndi maso.