2. Ndipo akuru a anthu onse a mapfuko onse a Israyeli anadziimika mu msonkhano wa anthu a Mulungu, anthu oyenda pansi zikwi mazana anai akusolola lupanga,
3. Ndipo ana a Benjamini anamva kuti ana a Israyeli adakwera kumka ku Mizipa, Nati ana a Israyeli, Nenani, coipa ici cinacitika bwanji?
4. Ndipo Mlevi, mwamuna wa mkazi anaphedwayo, anayankha nati, Ndinadza ine ku Gibeya wa Benjamini, ine ndi mkazi wanga wamng'ono, kugonako.
5. Nandiukira eni ace a Gibeya, nandizingira nyumba usiku; nafuna kundipha ine, namcitira coipa mkazi wanga wamng'ono, nafa iye,
6. Pamenepo ndinagwira mkazi wanga wamng'ono ndi kumgawa ndi kumtumiza m'dziko lonse la colowa ca Israyeli, pakuti anacita cocititsa manyazi ndi copusa m'lsrayeli.
7. Taonani, inu nonse, ndinu ana a Israyeli, mudzinenere mau ndi kudzipangira nokha kuno.
8. Ndipo anthu onse anauka ngati munthu mmodzi, ndi kuti, Palibe mmodzi wa ife adzamuka kuhema kwace, kapena kupambukira nyumba yace,
9. koma tsopano ici ndico tidzacitira Gibeya: tidzaukwerera ndi kulota maere.
10. Ndipo tidzatapa amuna khumi limodzi pa zana limodzi, mwa mapfuko onse a Israyeli; ndi zana limodzi pa zikwi cimodzi, ndi cikwi cimodzi pa zikwi khumi kutengera anthu kamba; kuti pakufika ku Gibeya wa Benjamini, aucitire monga mwa copusa conse unacita m'Israyeli.
11. Potero amuna onse a Israyeli anasonkhanira mudziwo, olunzika ngati munthu mmodzi.
12. Ndipo mapfuko a Israyeli anatuma anthu mwa pfuko lonse la Benjamini, ndi kuti, Coipa canji ici cinacitika mwa inu?
13. Ndipo tsopano perekani amunawo otama zopanda pace, okhala m'Gibeya, kuti tiwaphe, ndi kucotsera Israyeli coipaci. Koma Benjamini sanafuna kumvera mau a abale ao, ana a Israyeli.
14. Ndipo ana a Benjamini anasonkhana kucokera ku midzi kumka ku Gibeya, kuti aturuke kulimbana ndi ana a Israyeli.