Ndipo tsopano perekani amunawo otama zopanda pace, okhala m'Gibeya, kuti tiwaphe, ndi kucotsera Israyeli coipaci. Koma Benjamini sanafuna kumvera mau a abale ao, ana a Israyeli.