Oweruza 11:7-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo Yefita anati kwa akulu a Gileadi, Simunandida kodi, ndi kundicotsa m'nyumba ya atate wanga? ndipo mundidzeraoji tsopano pokhala muli m'kusauka?

8. Ndipo akuru a Gileadi ananena ndi Yefita, Cifukwa cace cakuti takubwerera tsopano ndico kuti umuke nafe ndi kucita nkhondo ndi ana a Amoni, nudzakhala mkuru wathu wa pa onse okhala m'Gileadi.

9. Ndipo Yefita anati kwa akuru a Gileadi, Mukaodifikitsanso kwathu kucita nkhondo ndi ana a Amoni, nakawapereka Yehova pamaso panga, ndidzakhala mkuru wanu kodi?

10. Ndipo akuru a Gileadi anati kwa Yefita, Yehova ndiye wakumvera pakati pa ife, tikapanda kucita monga momwe wanena.

11. Pamenepo Yefita anamuka ndi akuru a Gileadi, ndipo anthu anamuika mkuru wao ndi mtsogoleri wao; ndipo Yefita ananena mau ace onse pamaso pa Yehova ku Mizipa.

12. Ndipo Yefita anatuma mithenga kwa mfumu ya ana a Amoni, ndi kuti, Ndi ciani ndi Inu, ndi kuti Mwandidzera kuthira nkhondo dziko langa?

13. Ndipo mfumu ya ana a Amoni inati kwa mithenga ya Yefita, Cifukwa Israyeli analanda dziko langa pakukwera iye kucokera ku Aigupto, kuyambira Arinoni mpaka Yaboki, ndi mpaka Yordano; ndipo tsopano uodibwezere maikowa mwamtendere.

14. Ndipo Yefita anatumanso mithenga kwa mfumu ya ana a Amoni;

Oweruza 11