Oweruza 11:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yefita Mgileadi ndipo anali ngwazi yamphamvu, ndiye mwana wa mkazi wadama; koma Gileadi adabala Yefita.

2. Ndipo mkazi wa Gileadi anambalira ana amuna; koma atakula ana amuna a mkaziyo anampitikitsa Yefita, nanena naye, Sudzalandira colowa m'nyumba ya atate wako; pakuti ndiwe mwana wa mkazi wina.

3. Pamenepo Yefita anathawa abale ace, nakhala m'dziko la Tobu; ndipo anyamata opanda pace anasonkhana kwa Yefita, naturuka naye pamodzi.

4. Ndipo kunali, atapita masiku, ana a Amoni anacita nkhondo ndi Israyeli,

5. ndipo kunatero, pamene ana a Amoni anathira nkhondo pa Israyeli, akuru a Gileadi anamuka kutenga Yefita m'dziko la Tobu;

6. nati kwa Yefita, Tiye ukhale kazembe wathu kuti tilimbane ndi ana a Amoni.

Oweruza 11