Mateyu 9:27-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Ndipo popita Yesu kucokera kumeneko, anamtsata Iye anthu awiri akhungu, opfuula ndi kuti, Muticitire ife cifundo, mwana wa Davide.

28. Ndipo m'mene Iye analowa m'nyumbamo, akhunguwo anadza kwa Iye; ndipo Yesu anati kwa iwo, Mukhulupirira kodi kuti ndikhoza kucita ici? Anena kwa Iye, Inde, Ambuye.

29. Pomwepo anakhudza maso ao, nati, Cicitidwe kwa inu monga cikhulupiriro canu.

30. Ndipo maso ao anaphenyuka. Ndipo Yesu anawauzitsa Iwo, nanena, Yang'anirani, asadziwe munthu ali yense.

31. Koma iwo anaturukamo, nabukitsa mbiri yace m'dziko lonselo.

32. Ndipo pamene iwo analikuturuka, onani, anabwera naye kwa Iye munthu wosalankhula, wogwidwa ndi ciwanda.

33. Ndipo m'mene cinaturutsidwa ciwandaco, wosalankhulayo analankhula, ndipo makamu a anthu anazizwa, nanena, Kale lonse sicinaoneke comweco mwa Israyeli.

34. Koma Afarisi analinkunena, Aturutsa ziwanda ndi mphamvu zace za mfumu ya ziwanda.

35. Ndipo Yesu anayendayenda m'mizinda yonse ndi m'midzi, namaphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira uthenga wabwino wa Ufumuwo, naciritsa nthenda iri yonse ndi zofoka zonse.

36. Koma Iye, poona makamuwo, anagwidwa m'mtima ndi cisoni cifukwa ca iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.

37. Pomwepo ananena kwa ophunzira ace, Zotuta zicurukadi koma anchito ali owerengeka.

38. Cifukwa cace pempherani Mwini zotuta kuti akokose anchito kukututakwace.

Mateyu 9