Mateyu 26:12-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Pakuti mkaziyo, m'mene anathira mafuta awa pathupi panga, wandicitiratu ici pa kuikidwa kwanga.

13. Indetu ndinena kwa inu, kumene kuli konse uthenga uwu wabwino udzalalikidwa m'dziko lonse lapansi, ici cimene mkaziyo anacitaci cidzakambidwanso cikumbukiro cace.

14. Pomwepo mmodzi wa khumi ndi awiriwo, dzina lace Yudase Isikariote, anamuka kwa ansembe akuru,

15. nati, Mufuna kundipatsa ciani, ndipo ine ndidzampereka Iye kwa inu? Ndipo iwo anamwerengera iye ndalama zasiliva makumi atatu.

16. Ndipo kuyambira pamenepo iye anafunafuna nthawi yabwino yakuti ampereke Iye.

17. Ndipo tsiku loyamba la mkate wopanda cotupitsa, ophunzira anadza kwa Yesu, nati, Mufuna tikakonzere kuti Paskha, kuti mukadye?

18. Nati Iye, Mukani kumzinda kwa munthu wangana, mukati kwa iye, Mphunzitsi anena. Nthawi yanga yayandikirai ndidzadya Paskha kwanu pamodzi ndi ophunzira anga.

19. Ndipo ophunzira anacita monga Yesu anawauza, nakonza Paskha.

20. Ndipo pakufika madzulo, Iye analikukhala pacakudya pamodzi ndi ophunzira khumi ndi awiri;

21. ndipo m'mene analinkudya, Iye anati, Indetu ndinena kwa inu, mmodzi wa inu adzandipereka Ine.

22. Ndipo iwo anagwidwa ndi cisoni cacikuru, nayamba kunena kwa Iye mmodzi mmodzi, Kodi ndine, Ambuye?

23. Ndipo Iye anayankha nati, Iye amene asunsa pamodzi ndi Ine dzanja lace m'mbale, yemweyu adzandipereka Ine.

24. Mwana wa munthu acokatu, monga kunalembedwa za Iye; koma tsoka ali nalo munthu amene Mwana wa munthu aperekedwa ndi iye! kukadakhala bwino kwa munthuyo ngati sakadabadwa.

25. Ndipo Yudase, womperekayo anayankha nati, Kedi ndine, Rabi? Iye ananena kwa iye, Iwe watero.

26. Ndipo pamene iwo analinkudya, Yesu anatenga mkate, nadalitsa, naunyema; ndipo m'mene anapatsa kwa ophunzira, anati, Tengani, idyani; ici ndi thupi langa.

27. Ndipo pamene anatenga cikho, anayamika, napatsa iwo, nanena, Mumwere ici inu nonse,

Mateyu 26