15. Koma ansembe akuru ndi alembi, m'mene anaona zozizwitsa zomwe Iye anazicita, ndi ana alinkupfuula kuKacisiko kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide, anapsa mtima,
16. nanena kwa Iye, Mulinkumva kodi cimene alikunena awa? Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Inde: simunawerenga kodi, M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza?
17. Ndipo Iye anawasiya, naturuka m'mzinda, napita ku Betaniya, nagona kumeneko.
18. Ndipo mamawa, m'mene Iye analinkunkanso kumzinda, anamva njala,
19. Ndipo pakuona mkuyu umodzi panjira, anafika pamenepo, napeza palibe kanthu koma masamba okha okha; nati Iye kwa uwo, Sudzabalanso cipatso ku nthawi zonse. Ndipo pomwepo mkuyuwo unafota.
20. Ndipo ophunzira poona ici anazizwa, nati, Mkuyuwo unafota bwanji msanga?
21. Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Indedi ndinena kwa inu, Ngati mukhala naco cikhulupiriro, osakayika-kayika, mudzacita si ici ca pa mkuyu cokha, koma ngati mudzati ngakhale ku phiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nvania, cidzacitidwa.
22. Ndipo zinthu ziri zonse mukazifunsa m'kupemphera ndi kukhulupirira, mudzazilandira.
23. Ndipo m'mene Iye analowa m'Kacisi, ansembe akuru ndi akuru anthu anadza kwa Iye analikuphunzitsa, nanena, Mucita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere?
24. Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Inenso ndikufunsani mau amodzi, amene ngati muneliuza, Inenso ndikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizicita izi:
25. Ubatizo wa Yohane, ucokera kuti? Kumwamba kodi kapena kwa anthu? Koma iwo anafunsana wina ndi mnzace, kuti, Tikati, Kumwamba, Iye adzati kwa ife, Munalekeranji kumvera iye?
26. Koma tikati, Kwa anthu, tiopa khamulo la anthu; pakuti onse amuyesa Yohane mneneri.
27. Ndipo anamyankha Yesu, nati, Sitidziwa ife. Iyenso ananena nao, lnenso sindikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizicita izi.
28. Nanga mutani? Munthu anali cao ana awiri; nadza iye kwa woyamba nati, Mwanawe, kagwire lero nchito ku munda wampesa.
29. Koma iye anakana, nati, Sindifuna ine; koma pambuyo pace analapa mtima napita.